1 CIYAMBI cace ca Uthenga Wabwino wa Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu.
2 Monga mwalembedwa m'Yesaya mneneri,Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu,Amene adzakonza njira yanu;
3 Mau a wopfuula m'cipululu, Konzani khwalala la Ambuye, Lungamitsani njira zace;
4 Yohane anadza nabatiza m'cipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku cikhululukiro ca macimo.
5 Ndipo anaturuka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordano, poulula macimo ao.
6 Ndipo Yohane anabvala ubweya wa ngamila, ndi lamba lacikopa m'cuuno mwace, nadya dzombe ndi uci wa kuthengo.
7 Ndipo analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula lamba la nsapato zace ine.
8 Ndakubatizani inu ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.
9 Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kucokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane m'Yordano.
10 Ndipo pomwepo, alimkukwera poturuka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda:
11 ndipo mau anaturuka m'thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.
12 Ndipo pomwepo Mzimu anamkangamiza kunka kucipululu.
13 Ndipo anakhala m'cipululu masiku makumi anai woyesedwa ndi Satana; nakhala ndi zirombo, ndipo angelo anamtumikira.
14 Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira uthenga wabwino wa Mulungu,
15 nanena, Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani uthenga wabwino.
16 Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andreya, mbale wace wa Simoni, alinkuponya psasa m'nyanja; pakuti anali asodzi.
17 Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.
18 Ndipo pomwepo anasiya makoka ao, namtsata Iye.
19 Ndipo atapita patsogolo pang'ono, anaona Yakobo, mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace, iwonso anali m'combo nakonza makoka ao.
20 Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedayo m'combomo pamodzi ndi anchito olembedwa, namtsata.
21 Ndipo iwo analowa m'Kapemao; ndipo pomwepo pa dzuwa la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa,
22 Ndipo anazizwa ndi ciphunzitso cace; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi.
23 Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anapfuula iye
24 kuti, Tiri ndi ciani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife? Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.
25 Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli cete, nuturuke mwa iye.
26 Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kupfuula ndi mau akuru, unaturuka mwa iye.
27 Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ici nciani? ciphunzitso catsopano! ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye.
28 Ndipo mbiri yace inabuka pompaja ku dziko lonse la Galileya lozungulirapo.
29 Ndipo pomwepo, poturuka m'sunagoge, iwo analowa m'nyumba ya Simoni ndi Andreya pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane,
30 Ndipo mpongozi wace wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za iye:
31 ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.
32 Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda.
33 Ndipo mudzi wonse unasonkhana pakhomo.
34 Ndipo anaciritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundu mitundu, naturutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalola ziwandazo zilankhule, cifukwa zinamdziwa Iye.
35 Ndipo m'mawa mwace anauka usikusiku, naturuka namuka kucipululu, napemphera kumeneko.
36 Ndipo Simoni ndi anzace anali naye anamtsata,
37 nampeza, nanena naye, Akufunani inu anthu onse.
38 Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, ku midzi iri pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera nchito imene.
39 Ndipo analowa m'masunagoge mwao m'Galileya monse, nalalikira, naturutsa ziwanda.
40 Ndipo anadza kwa Iye wodwala khate, nampempha Iye, namgwadira, ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza.
41 Ndipo Yesu anagwidwa cifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.
42 Ndipo pomwepo khate linamcoka, ndipo anakonzedwa.
43 Ndipo anamuuzitsa, namturutsa pomwepo,
44 nanena naye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu ali yense: koma muka, ukadzionetse kwa wansembe, nupereke pa makonzedwe ako 1 zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo.
45 Koma 2 iye anaturuka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanadziwa kulowansopoyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a ku malo onse.