Mateyu 28 BL92

Yesu auka kwa akufa

1 Ndipo popita dzuwa la Sabata, mbanda kuca, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Mariya wa Magadala, ndi Mariya winayo, kudzaona manda.

2 Ndipo onani, panali cibvomezi cacikuru; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pace.

3 Kuonekera kwace kunali ngati mphezi, ndi cobvala cace coyeretsa ngati matalala;

4 ndipo ndi kuopsa kwace alondawo ananthunthumira, nakhala ngati anthu akufa.

5 Koma mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, Musaope inu; pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene anapacikidwa.

6 Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye.

7 Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ace, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.

8 Ndipo iwo anacoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukuru, nathamanga kukauza ophunzira ace.

9 Ndipo onani, Yesu anakomana nao, nanena, Tikuoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ace, namgwadira.

10 Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.

Mau omveka mwa Ayuda

11 Ndipo pameneiwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe akuru zonse zimene zinacitidwa.

12 Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akuru, anakhala upo, napatsa asilikariwo ndalama zambiri,

13 nati, Kazinenani, kuti ophunzira ace anadza usiku, namuba Uja m'mene ife tinali m'tulo.

14 Ndipo ngati ici cidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhawa.

15 Ndipo iwo analandira ndalamazo, nacita monga anawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe.

Yesu aoneka m'Galileya

16 Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangifa.

17 Ndipo pamene anamuona Iye, anamlambira; koma ena anakayika.

18 Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pa dziko lapansi.

19 Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:

20 ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira cimariziro ca nthawi ya pansi pano.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28