1 Pomwepo anadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, ocokera ku Yerusalemu, nati,
2 Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? pakuti sasamba manja pakudya.
3 Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu cifukwa ca miyambo yanu?
4 Pakuti Mulungu anati,Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo,Wakunenera atate wace ndi amace zoipa, afe ndithu.
5 Koma inu munena, Amene ali yense anena kwa atate wace kapena kwa amace, Ico ukanathandizidwa naco, neoperekedwa kwa Mulungu;
6 iyeyo sadzalemekeza atate wace. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu cifukwa ca miyambo yanu.
7 Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndikuti,
8 Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao;Koma mtima wao uli kutari ndi Ine.
9 Koma andilambira Ine kwacabe,Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.
10 Ndipo Iye anaitana makamuwo nati kwa iwo, Imvani, nimudziwitse;
11 si cimene cilowa m'kamwa mwace ciipitsa munthu; koma cimene cituruka m'kamwa mwace, ndico ciipitsa munthu.
12 Pomwepo anadza ophunzira, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva conenaco?
13 Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzala, udzazulidwa.
14 Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.
15 Ndipo Petro anayankha nati kwa Iye, Mutifotokozere ife fanizoli.
16 Ndipo Iye anati, Kodi inunso mukhala cipulukirire?
17 Simudziwa kodi kuti zonse zakulowa m'kamwa zipita m'mimba, ndipo zitayidwa kuthengo?
18 Koma zakuturuka m'kamwa zicokera mumtima; ndizo ziipitsa munthu.
19 Pakuti mumtima mucokera maganizo oipa, zakupha, zacigololo, zaciwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;
20 izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthuai.
21 Ndipo Yesu anaturukapo napatukira ku mbali za Turo ndi Sidoni.
22 Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anaturuka m'malire, napfuula, nati, Mundicitire ine cifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi ciwanda.
23 Koma Iye sanamyankha mau amodzi. Ndipo ophunzira ace anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti apfuula pambuyo pathu.
24 Ndipo Iye anayankha, nati, Sindinatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotayika za banja la Israyeli.
25 Koma iye anadza, namgwadira Iye, nanena, Ambuye, ndithangateni ine.
26 Ndipo Iye anayankha, nati, Sicabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuuponyera tiagaru.
27 Koma iye anati, Etu, Ambuye, pakutinso tiagaru timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye ao.
28 Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, cikhulupiriro cako ndi cacikuru; cikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wace anacira nthawi yomweyo.
29 Ndipo Yesu anacoka kumeneko, nadza ku nyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo.
30 Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nao opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ace: ndipo Iye anawaciritsa;
31 kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nacira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israyeli.
32 Ndipo Yesu anaitana ophunzira ace, nati, Mtima wanga ucitira cifundo khamu la anthuwa, pakuti ali cikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira,
33 Ndipo ophunzira ananena kwa Iye, Tiione kuti mikate yotere m'cipululu yakukhutitsa unyinji wotere wa anthu?
34 Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo anati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang'ono.
35 Ndipo Iye analamulira anthuwo akhale pansi onse;
36 natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu.
37 Ndipo onsewa anadya, nakhuta: ndipo anatola makombo otsala malicero asanu ndi awiri odzala.
38 Ndipo anadyawo anali amuna zikwi zinai kuwaleka akazi ndi ana.
39 Ndipo m'mene Iye anauza makamuwo amuke, analowa m'ngalawa, nafika m'malire Magadani.