1 Ndipo parnene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, ku phiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri,
2 nanena kwa iwo, Mukani ku mudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza buru womangidwa, ndi mwana wace pamodzi nave, masulani iwo, mudze nao kwa Ine.
3 Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asowa iwo, Ndipo pomwepo adzawatumiza.
4 Ndipo ici cinatero, kuti cikacitidwe conenedwa ndi mneneri kuti,
5 Tauzani mwanawamkazi wa Ziyoni,Taona, Mfumu yako idza kwa iwe,Wofatsa ndi wokwera pa buru,Ndi pa kaburu, mwana wa nyama yonyarnula katundu.
6 Ndipo ophunzirawo anamuka, nacita monga Yesu anawauza;
7 nabwera ndi buru ndi mwana wace, naika pa iwo zobvala zao, nakhala Iye pamenepo.
8 Ndipo ambirimbiri a mpingowo anayala zobvala zao panjira; Ndipo ena anadula nthambi za mitengo, naziyala m'njirarno.
9 Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inapfuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana m'Kumwambamwamba!
10 Ndipo m'mene adalowa m'Yerusalemu mudzi wonse unasokonezeka, nanena, ndani uyu?
11 Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.
12 Ndipo Yesu analowa ku Kacisi wa Mulungu naturutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;
13 nanena kwa iwo, Calembedwa, Nyumba yanga idzanenedwa nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la acifwamba.
14 Ndipo anadza kwa Iye kuKacisiko akhungu ndi opunduka miyendo, naciritsidwa.
15 Koma ansembe akuru ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazicita, ndi ana alinkupfuula kuKacisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,
16 nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi cimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenga kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?
17 Ndipo Iye anawasiya, naturuka m'mzinda, napita ku Betaniya, nagona kumeneko.
18 Ndipo mamawa, m'mene Iye analinkunkanso kumzinda, anamva njala,
19 Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okha okha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso cipatso ku nthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota.
20 Ndipo ophunzira poona ici anazizwa, nati, Mkuyuwo unafota bwanji msanga?
21 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala naco cikhulupiriro, osakayika-kayika, mudzacita si ici ca pa mkuyu cokha, koma ngati mudzati ngakhale ku phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nvania, cidzacitidwa.
22 Ndipo zinthu ziri zonse mukazifunsa m'kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira.
23 Ndipo m'mene Iye analowa m'Kacisi, ansembe akuru ndi akuru anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Mucita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?
24 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati muneliuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizicita izi:
25 Ubatizo wa Yohane, ucokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu? Koma iwo anafunsana wina ndi mnzace, kuti, Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye?
26 Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.
27 Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, lnenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizicita izi.
28 Nanga mutani? Munthu anali cao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero nchito ku munda wampesa.
29 Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pace analapa mtima napita.
30 Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anabvomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapita.
31 Ndani wa awiriwo anacita cifuniro ca atate wace? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi aciwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.
32 Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya cilungamo, ndipo simunamveraiye; koma amisonkho ndi akazi aciwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munaciona, simunalapa pambuyo pace, kuti mumvere iye.
33 Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wamphesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.
34 Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ace kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zace.
35 Ndipo olimawo anatenga akapolo ace, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala.
36 Anatumizanso akapolo ena, akucuruka oposa akuyambawa; ndipo anawacitira iwo momwemo.
37 Koma pambuyo pace anatumiza kwa iwo mwana wace, nati, Adzacitira mwana wanga ulemu.
38 Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzace, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga colowa cace.
39 Ndipo anamtenga iye, namponya kunja kwa munda, namupha.
40 Tsono atabwera mwini munda, adzacitira olimawo ciani?
41 Iwo ananena kwa Iye, Adzaononga koipa oipawo, nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zace.
42 Yesu ananena kwa iwo, 1 Kodi simunawerenga konse m'malembo,Mwala umene anaukana omanga nyumbaWomwewu unakhala mutu wa pangondya:ici cinacokera kwa Ambuye,Ndipo ciri cozizwitsa m'maso mwathu?
43 Cifukwa cace ndinena kwa inu, 2 Ufumu wa Mulungu udzacotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zace.
44 Ndipo 3 iye wakugwa pa mwala uwu adzaphwanyika; koma pa iye amene udzamgwera, udzampera iye.
45 Ndipo ansembe akuru ndi Afarisi, pakumva mafanizo ace, anazindikira kuti alikunena za iwo.
46 Ndipo pamene anafuna kumgwira, anaopa makamu a anthu, 4 cifukwa anamuyesa mneneri.