1 Ndipo Yesu anaturuka kuKacisi; ndipo ophunzira ace anadza kudzamuonetsa cimangidwe ca Kacisiyo.
2 Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzace, umene sudzagwetsedwa.
3 Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? ndipo cizindikiro ca kufika kwanu nciani, ndi ca mathedwe a nthawi ya pansi pano?
4 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu.
5 Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Kristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.
6 Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma citsiriziro sicinafike.
7 Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zibvomezi m'malo akuti akuti.
8 Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.
9 Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, cifukwa ca dzina langa.
10 Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzace, nadzadana wina ndi mnzace.
11 Ndipo aneneri onama ambiri adzauka, nadzasokeretsaanthuambiri.
12 Ndipo cifukwa ca kucuruka kwa kusayeruzika, cikondano ca anthu aunyinji cidzazirala.
13 Koma iye wakulimbika cilimbikire kufikira kucimariziro, yemweyo adzapulumuka.
14 Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu h mitundu yonse; ndipo pomwepo cidzafika cimariziro.
15 Cifukwa cace m'mene mukadzaona conyansa ca kupululutsa, cimene cidanenedwa ndi Danieli mneneri, citaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)
16 pomwepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri:
17 iye ali pamwamba pa chindwi, asatsikire kunyamula za m'nyumba mwace;
18 ndi iye wa m'munda asabwere kutenga copfunda cace.
19 Koma tsoka ali nalo iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana m'masiku awo!
20 Ndipo pempherani kuti kuthawa kwanu kusakhale pa nyengo yacisanu, kapena pa Sabata;
21 pakuti pomwepo padzakhala masauko akuru, monga sipadakhale otero kuyambira ciyambi ca dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.
22 Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu ali yense: koma cifukwa ca osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.
23 Pomwepo munthu akanena kwa inu, Onani, Kristu ali kuno, kapena uko musambvomereze;
24 cifukwa Akristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikuru ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.
25 Cifukwa cace akanena kwa inu, Onani, Iye ali m'cipululu; musamukeko.
26 Onani, ali m'zipinda; musabvomereze.
27 Pakuti monga mphezi idzera kum'mawa, nionekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwace kwa Mwana wa munthu.
28 Kumene kuli konse uli mtembo, miimba Idzasonkhanira konko.
29 Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwace, ndi nyenyezi zidzagwa kucokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:
30 ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo cizindikiro ca Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pacifuwa, nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukuru.
31 Ndipo Iye adzatumiza angelo ace ndi kulira kwakukuru kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ace ku mphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ace ena.
32 Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lace; pamene tsopano nthambi yace iri yanthete, nipuka masa-i mba ace, muzindikira kuti dzinja liyandikira;
33 comweconso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti Iye ali pafupi, inde pakhomo.
34 Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kucoka, kufikira zinthu zonsezi zidzacitidwa.
35 Thambo ndi dziko lapansi zidzacoka, koma mau anga sadzacoka ai.
36 Koma za tsiku ilo ndi nthawi yace sadziwa munthu ali yense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.
37 Ndipo 1 monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwace kwa Mwana wa munthu.
38 Pakuti monga m'masiku aja, cisanafike cigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'cingalawa,
39 ndipo iwo sanadziwa kanthu, kufikira kumene cigumula cinadza, cinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwace kwa Mwana wa munthu.
40 Pomwepo 2 adzakhala awiri m'munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa:
41 awiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.
42 3 Cifukwa cace dikirani, pakuti simudziwa tsiku lace lakufika Ambuye wanu.
43 Koma 4 dziwani ici, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yace ibooledwe.
44 Cifukwa cace 5 khalani inunso okonzekeratu; cifukwa munthawi m'mene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.
45 6 Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wace anamkhazika woyang'anira banja lace, kuwapatsa zakudya pa nthawi yace?
46 Wodala kapolo amene mbuye wace, pakufika, adzampeza iye alikucita cotero.
47 Indetu, ndinena kwa inu, kuti 7 adzamkhazika iye woyang'anira zinthu zace zonse.
48 Koma kapolo woipa akanena mumtima mwace, Mbuye wanga wacedwa;
49 nadzayamba kupanda akapolo anzace, nadya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera;
50 mbuye wa kapoloyo adzafika tsiku losamuyembekeza iye, ndi nthawi yosadziwa iye,
51 nadzamdula, nadzaika pokhala pace ndi anthu onyenga; 8 pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano.