Mateyu 26 BL92

Akuru a Ayuda apangana amgwire Yesu

1 Ndipo panali pamene Yesu anatha mau onse amenewa, anati kwa ophunzira ace,

2 Mudziwa kuti akapita masiku awiri, Paskha ufika, ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kupacikidwa pamtanda.

3 Pomwepo anasonkhana ansembe akuru, ndi akuru a anthu, ku bwalo la mkuru wa ansembe, dzina lace Kayafa;

4 nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi cinyengo, namuphe.

5 Koma ananena iwo, Pa dzuwa la cakudya iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.

Yesu m'nyumba va Simoni wakhate

6 Ndipo pamene Yesu anali m'Betaniya, m'nyumba ya Simoni wakhate,

7 anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa yaalabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatari, nawatsanulira pamutu pace, m'mene Iye analikukhala pacakudya.

8 Koma m'mene ophunzira anaona, anada mtima, nanena, Cifukwa ninji kuononga kumeneku?

9 Pakuti mafuta awa akadagulitsa ndalama zambiri, ndi kuzipatsa anthu aumphawi.

10 Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumbvutiranji mkaziyu? popeza andicitira Ine nchito yabwino.

11 Pakuti nthawi zonse muli nao aumphawi pamodzi nanu; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.

12 Pakuti mkaziyo, m'mene anathira mafuta awa pathupi panga, wandicitiratu ici pa kuikidwa kwanga.

13 Indetu ndinena kwa inu, kumene kuli konse uthenga uwu wabwino udzalalikidwa m'dziko lonse lapansi, ici cimene mkaziyo anacitaci cidzakambidwanso cikumbukiro cace.

Mphotho ya kumpereka Yesu

14 Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lace Yudase Isikariote, anamuka kwa ansembe akuru,

15 nati, Mufuna kundipatsa ciani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu.

16 Ndipo kuyambira pamenepo iye anafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye.

Paskha wotsiriza, Mgonero wa Ambuye

17 Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda cotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paskha, kuti mukadye?

18 Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wangana, mukati kwa iye, Mphunzitsi anena. Nthawi yanga yayandikirai ndidzadya Paskha kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.

19 Ndipo ophunzira anacita monga Yesu anawauza, nakonza Paskha.

20 Ndipo pakufika madzulo, Iye analikukhala pacakudya pamodzi ndi ophunzira khumi ndi awiri;

21 ndipo m'mene analinkudya, Iye anati, Indetu ndinena kwa inu, mmodzi wa inu adzandipereka Ine.

22 Ndipo iwo anagwidwa ndi cisoni cacikuru, nayamba kunena kwa Iye mmodzi mmodzi, Kodi ndine, Ambuye?

23 Ndipo Iye anayankha nati, Iye amene asunsa pamodzi ndi Ine dzanja lace m'mbale, yemweyu adzandipereka Ine.

24 Mwana wa munthu acokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa munthu aperekedwa ndi iye! kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.

25 Ndipo Yudase, womperekayo anayankha nati, Kedi ndine, Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero.

26 Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ici ndi thupi langa.

27 Ndipo pamene anatenga cikho, anayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ici inu nonse,

28 pakuti ici ndici mwazi wanga wa pangano, wothiridwa cifukwa ca anthu ambiri ku kucotsa macimo.

29 Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso cipatso ici campesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa catsopano, pamodzi ndi inu, mu Ufumu wa Atate wanga.

30 Ndipo pamene anayimba nyimbo, anaturuka kunka ku phiri la Azitona.

Yesu acenjeza Petro

31 Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa cifukwa ca Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa,Ndidzakantha mbusa,Ndipo zidzabalalikaNkhosa za gulu.

32 Koma nditauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.

33 Koma Petro ananena kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa cifukwa ca Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse.

34 Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.

35 Petro ananena kwa Iye, Ngakhale ine ndikafa ndi Inu, sindidzakukanani Inu iai. Anateronso ophunzira onse.

Yesu m'Getsemane

36 Pomwepo Yesu anadza ndi iwo ku malo ochedwa Getsemane, nanena kwa ophunzira ace, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.

37 Ndipo anatenga Petro ndi ana awiria Zebedayo pamodzi naye, nayamba kugwidwa ndi cisoni ndi kuthedwa nzeru.

38 Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uti wozingidwa ndi cisoni ca kufika naco kuimfa; khalani pano mucezere pamodzi ndi Ine.

39 Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yace pansi, napemphera, nati, Atate, ngati nkutheka, cikho ici cindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma lou.

40 Ndipo anadza kwa ophunzira, nawapeza iwo ali m'tulo, nanena kwa Petro, Nkutero kodi? simukhoza kucezera ndi Ine mphindi imodzi?

41 Cezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uti wakufuna, koma thupi liri lolefuka.

42 Anamukanso kaciwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ici sicingandipitirire, koma ndimwere ici, kufuna kwanu kucitidwe.

43 Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali m'tulo, pakuti zikope zao zinalemera ndi tulo.

44 Ndipo anawasiyanso, napemphera kacitatu, nateronso mau omwewo.

45 Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa munthu aperekedwa m'manja ocimwa.

46 Ukani, timuke; taonani, iye wakundipereka wayandikira.

Amgwira Yesu

47 Ndipo Iye ali cilankhulire, onani, Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikuru la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kucokera kwa ansembe akuru ndi akuru a anthu.

48 Koma wompereka Iye anawapatsa cizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona ndiyeyo, mumgwire Iye.

49 Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuoneni, Rabi; nampsompsonetsa.

50 Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji: iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye.

51 Ndipo onani, mmodzi wa iwo anali pamodzi ndi Yesu, anatansa dzanja lace, nasolola Iupanga lace, nakantha kapolo wa mkuru wa ansembe, nadula khutu lace.

52 Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza Iupanga lako m'cimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi Iupanga,

53 Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri?

54 Koma pakutero malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera comweco?

55 Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munaturukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wacifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala m'Kacisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwira.

56 Koma izi zonse zinacitidwa, kuti 1 zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.

Yesu ku bwalo la akuru a Ayuda

57 Ndipo iwo akugwira Yesu anaaka naye kwa Kayafa, mkuru wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akuru omwe.

58 Koma Petro anamtsata kutari, kufikira ku bwalo la mkuru wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone cimariziro.

59 Ndipo ansembe akuru ndi akuru mirandu onse mafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;

60 koma sanaupeza zingakhale 2 mboni zonama zambiri zinadza. Koma pambuyo pace anadza awiri,

61 nati, Uyu ananena kuti, 3 Ndikhoza kupasula Kacisi, ndi kummanganso masiku atatu.

62 Ndipo mkuru wa ansembe anaimirira, nati kwa Iye, Subvomera kanthu kodi? nciani ici cimene awa akunenera Iwe?

63 Koma 4 Yesu anangokhala cete. Ndipo mkuru wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Kristu, Mwana wa Mulungu.

64 Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, 5 Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa munthu ali kukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.

65 Pomwepo mkuru wa ansembe 6 anang'amba zobvala zace, nati, Acitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? onani, tsopano mwamva mwanowo;

66 muganiza bwanji? lwo anayankha nati, 7 Ali woyenera kumupha,

67 8 Pomwepo iwo anathira malobvu pankhope pace, nambwanyula Iye; ndipo ena anampanda kofu,

68 nati, 9 Utilote ife, Kristu Iwe; wakumenya Iwe ndani?

Petro akana Yesu

69 Ndipo 10 Petro adakhala pabwato: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.

70 Koma iye anakana pamaso pa anthu onse, kuti, Cimene unena sindicidziwa.

71 Ndipo pamene iye anaturuka kunka kucipata, mkazi wina anamuona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo.

72 Ndipo anakananso ndi cilumbiro, kuti, Sindidziwa munthuyo.

73 Ndipo popita nthawi yaing'ono, iwo akuimapo anadza, nati kwa Petro, Zoonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe.

74 11 Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira.

75 Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, 12 Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anaturukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28