1 Yang'anirani kuti musacite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa Kumwamba.
2 Cifukwa cace pamene pali ponse upatsa mphatso zacifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amacita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.
3 Koma iwe popatsa mphatso zacifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe cimene licita dzanja lako lamanja;
4 kotero kuti mphatso zako zacifundo zikhale zam'tseri; ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
5 Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; cifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.
6 Koma iwe popemphera, Iowa m'cipinda cako, nutseke citseko cako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
7 Ndipo popemphera musabwereze-bwereze cabe iai, monga amacita anthu akunja, cifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhula-lankhula kwao.
8 Cifukwa cace inu musafanane nao: pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha Iye.
9 Cifukwa cace pempherani inu comweci:Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.
10 Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kucitidwe, monga Kumwamba comweco pansi pano.
11 Mutipatse ife lero cakudya cathu calero.
12 Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu.
13 Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.
14 Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba.
15 Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.
16 Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yacisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alimkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.
17 Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako:
18 kuti usaonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma kwa Atate wako ali m'tseri: ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
19 Musadzikundikire nokha cuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba:
20 koma mudzikundikire nokha cuma m'Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba;
21 pakuti kumene kuli cuma cako, komwe udzakhala mtima wakonso.
22 Diso ndilo nyali ya thupi; cifukwa cace ngati diso lako liri la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa.
23 Koma ngati diso lako liri loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa. Cifukwa cace ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukuru ndithu!
24 Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma.
25 Cifukwa cace ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, cimene mudzadya ndi cimene mudzamwa; kapena thupi lanu, cimene mudzabvala. Kodi moyo suli woposa cakudya, ndi thupi loposa cobvala?
26 Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?
27 Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wace mkono umodzi?
28 Ndipo muderanji nkhawa ndi cobvala? Tapenyetsani maluwa a kuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa nchito, kapena sapota:
29 koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wace wonse sanabvala monga limodzi la amenewa.
30 Koma ngati Mulungu abveka cotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi mawa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?
31 Cifukwa cace musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya ciani? kapena, Tidzamwa ciani? kapena, Tidzabvala ciani?
32 Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo.
33 Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
34 Cifukwa cace musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha, Zikwanire tsiku zobvuta zace.