Mateyu 5 BL92

Ciphunzitso ca paphiri Madalitso

1 Ndipo m'mene Iye anaona makamu, anakwera m'phiri; ndipo m'mene Iye anakhala pansi, anadza kwa Iye ophunzira ace;

2 ndipo anatsegula pakamwa, nawaphunzitsa iwo, nati:

3 Odala ali osauka mumzimu; cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.

4 Odala ali acisoni; cifukwa adzasangalatsidwa.

5 Odala ali akufatsa; cifukwa adzalandira dziko lapansi.

6 Odala ali akumva njala ndi ludzu la cilungamo; cifukwa adzakhuta.

7 Odala ali akucitira cifundo; cifukwa adzalandira cifundo.

8 Odala ali oyera mtima; cifukwa adzaona Mulungu.

9 Odala ali akucita mtendere; cifukwa adzachedwa ana a Mulungu.

10 Odalaaliakuzunzidwacifukwa ca cilungamo: cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.

11 Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa ziri zonse cifukwa ca Ine.

12 Sekerani, sangalalani: cifukwa mphotho yanu ndi yaikuru m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.

Ophunzira ace ali mcere wa dziko ndi kuunika kwa dziko

13 Inu ndinu mcere wa dziko lapansi; koma mcerewo ngati uka: sukuluka, adzaukoleretsa ndi ciani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.

14 Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika.

15 Kapena sayatsa nyali, ndi kuibvundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa coikapo cace; ndipo iunikira onse: ali m'nyumbamo.

16 Comweco muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona nchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Makwaniridwe a Malamulo ndi Aneneri

17 Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula cilamulo kapena ane, neri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa.

18 Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kace kamodzi sikadzaeokera kucilamulo, kufikira zitacitidwa zonse.

19 Cifukwa cace yense wakumasula limodzi la malangizo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu comweco, adzachulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakucita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzachulidwa wamkuru mu Ufumu wa Kumwamba.

20 Pakuti ndinena ndi inu, ngati cilungamo canu sicicuruka coposa ca alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

21 Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu:

22 koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wace wopanda cifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wace, Wopanda pace iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akuru: koma amene adzati, Citsiru iwe: adzakhala wopalamula gehena wamoto.

23 Cifukwa cace ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe,

24 usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nucoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.

25 Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikari, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende.

26 Indetu ndinena ndi iwe, sudzaturukamo konse, koma utalipa kakobiri kakumariza ndiko.

27 Munamva kuti kunanenedwa, Usacite cigololo;

28 koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kucita naye cigololo mumtima mwace.

29 Koma 1 ngati diso lake lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti cimodzi ca ziwalo zako cionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse m'gehena.

30 Ndipo 2 ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti cimodzi ca ziwalo zako cionongeke, losamuka thupi lako lonse kugehena.

31 Kunanenedwanso, Yense wakucotsa mkazi wace 3 ampatse iye cilekaniro:

32 koma Ine ndinena kwa inu, kuti 4 yense wakucotsa mkazi wace, kosati cifukwa ca cigololo, amcititsa cigololo: ndipo amene adzakwata wocotsedwayo acita cigololo.

33 Ndiponso, munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, 5 Usalumbire konama, koma udzapereka kwa Ambuye zolumbira zako:

34 koma Ine ndinena kwa inu, 6 Musalumbire konse, kapena kuchula Kumwamba, cifukwa kuli cimpando ca Mulungu;

35 7 kapena kuchula dziko lapansi, cifukwa liri popondapo mapazi ace; kapena kuchula Yerusalemu, cifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikurukuru.

36 8 Kapena usalumbire ku mutu wako, cifukwa sungathe kuliyeretsa mbu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi.

37 9 Kama manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo coonjezedwa pa izo cicokera kwa woipayo.

38 Munamva kuti kunanenedwa, 10 Diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino:

39 koma ndinena kwa inu, 11 Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako Lamanja, umtembenuzire linanso.

40 Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso copfunda cako.

41 Ndipo 12 amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri.

42 Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye 13 wofuna kukukongola usampotolokere.

43 Munamva kuti kunanenedwa, 14 Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako:

44 koma Ine ndinena kwa inu, 15 Kondanani nao adani anu, ndi 16 kupempherera iwo akuzunza inu;

45 kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; cifukwa Iye amakwezera dzuwa lace pa oipa ndi pa abwino, namabvumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.

46 Cifukwa kuti 17 ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? kodi angakhale amisonkho sacita comweco?

47 Ndipo ngati mulankhula abale anu okha okha, mucitanji coposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sacita comweco?

48 Cifukwa cace inu 18 mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28