1 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wace, napita nao pa okha pa phiri lalitari;
2 ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yace inawala monga dzuwa, ndi zobvala zace zinakhala zoyera mbu monga kuwala.
3 Ndipo onani, Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo, alinkulankhula ndi Iye.
4 Ndipo Petro anayankha, nati kwa Yesu, Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano; ngati mulola ndidzamanga pane misasa itatu; umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.
5 Akali cilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphi mba iwo: ndipo onani, mau alikunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.
6 Ndipo pamene ophunzira anamva, anagwa nkhope zao pansi, naopa kwakukuru.
7 Ndipo Yesu anadza, nawakhudza nati, Ukani, musaopa,
8 Ndipo iwo, pokweza maso ao sanaona munthu, koma Yesu yekha.
9 Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalangiza iwo kuti, Musakauze munthu coonekaco, kufikira Mwana wa munthu adadzauka kwa akufa.
10 Ndipo ophunzira ace anamfunsa, nanena, Ndipo bwanji alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza?
11 Ndipo Iye anayankha, nati, Eliya akudzatu, nadzabwezera zinthu zonse;
12 koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwa iye, koma anamcitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo conconso Mwana wa munthu adzazunzidwa ndi iwo.
13 Pomwepo ophunzira anazindikira kuti analankhula nao za Yohane Mbatizi.
14 Ndipo pamene iwo anadza ku khamu la anthu, kunafika kwa Iye munthu, namgwadira Iye, nati,
15 Ambuye, citirani mwana wanga cifundo; cifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawiri kawiri pamoto, ndi kawiri kawiri m'madzi.
16 Ndipo ndinadza naye kwa ophunzira anu, koma iwo sanathe kumciritsa.
17 Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? ndidzalekerera inu nthawi yanji? mudze naye kwa Ine kuno.
18 Ndipo. Yesu anamdzudzula; ndipo ciwanda cinaturuka mwa iye; ndipo mnyamatayo anacira kuyambira nthawi yomweyo.
19 Pamenepo ophunzira anadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, Nanga ife sitinakhoza bwanji kuciturutsa?
20 Ndipo Iye ananena kwa iwo, Cifukwa cikhulupiriro canu ncacing'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala naco cikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakulakani kosacitika. [
21 ]
22 Ndipo m'mene anali kutsotsa m'Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa munthu adzaperekedwa m'manja a anthu;
23 ndipo adzamupha Iye, ndipo Iye adzauka tsiku lacitatu. Ndipo iwo anali ndi cisoni cacikuru.
24 Ndipo pofika ku Kapernao arnene aja akulandira ndalama za kukacisi anadza kwa Petro nati, Kodi Mphunzitsi wanu sapereka rupiyalo?
25 Iye anabvomera, Apereka, Ndipo polowa iye m'nyumba, Yesu anatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? kwa ana ao kodi, kapena kwa akunja?
26 Ndipo m'mene iye anati, Kwa akunja, Yesu ananena kwa iye, Cifukwa cace anawo ali aufulu.
27 Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pace udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamtu pa iwe ndi Ine.