Mateyu 12 BL92

Yesu mbuye wa Sabata

1 Nyengo imeneyo Yesu anapita tsiku la Sabata pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ace anali ndi njala, nayamba kubudula ngala, nadya.

2 Koma Afarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu acita cosaloleka tsiku la Sabata.

3 Koma Iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenga cimene anacicita Davide, pamene anali ndi njala, ndi iwo amene anali naye?

4 kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okha okha.

5 Kapena simunawerenga kodi m'cilamulo, kuti tsiku la Sabata ansembe m'Kacisi amaipitsa tsiku la Sabata, nakhala opanda cimo?

6 Koma ndinena kwa inu, kuti wakuposa Kacisiyo ali pompano.

7 Koma mukadadziwa nciani ici:Ndifuna cifundo, si nsembe ai; simukadaweruza olakwa iwo osacimwa,

8 pakuti Mwana wa munthu ali mwini tsiku la Sabata.

Yesu aciritsa wa dzanja lopuwala

9 Ndipo Iye anacokera pamenepo, nalowa m'sunagoge mwao;

10 ndipo onani, munali munthu wa dzanja lopuwala, Ndipo anamfunsitsa Iye, ndi kuti, Nkuloleka kodi kuciritsa tsiku la Sabata? kuti ampalamulitse mlandu.

11 Koma Iye anati kwa iwo, Munthu ndani wa inu, amene ali nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m'dzenje tsiku la Sabata, kodi sadzaigwira, ndi kuiturutsa?

12 Nanga kuposa kwace kwa munthu ndi nkhosa nkotani! Cifukwa ca ici nkuloleka kucita zabwino tsiku la Sabata.

13 Pomwepo ananena Iye kwa munthuyo, Tansa dzanja Lako. Ndipo iye analitansa, ndipo linabwezedwa lamoyo longa linzace.

14 Ndipo Afarisi anaturuka, nakhala upo womcitira Iye mwa kumuononga.

15 Koma Yesu m'mene anadziwa, anacokera kumeneko: ndipo anamtsata Iye anthu ambiri; ndipo Iye anawaciritsa iwo onse,

16 nawalimbitsira mau kuti asamuulule Iye;

17 kuti cikacitidwe conenedwa ndi Yesaya mneneri uja, kuti,

18 Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha,Wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye;Pa Iye ndidzaika Mzimu wanga,Ndipo Iye adzalalikira ciweruzo kwa akunja.

19 Sadzalimbana, sadzapfuula;Ngakhale mmodzi sadzamva mau ace m'makwalala;

20 Bango lophwanyika sadzalityola,Ndi nyali yofuka sadzaizima,Kufikira Iye adzatumiza ciweruzo cikagonjetse,

21 Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lace.

Mwano wa Afarisi

22 Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi ciwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamciritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya.

23 Ndipo makamu onse a anthu anazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi?

24 Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samaturutsa ziwanda koma ndi mphamvu yace ya Beelzebule, mkuru wa ziwanda.

25 Ndipo Yesu anadziwa maganizo ao, nati kwa iwo, Ufumu uti wonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mudzi uti wonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala;

26 ndipo ngati Satana amaturutsa Satana, iye agawanika pa yekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wace?

27 Ndipo ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi mphamvu yace ya Beelzebule, ana anu amaziturutsa ndi mphamvu ya yani? cifukwa cace iwo adzakhala oweruza anu.

28 Koma ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi mphamvu yace ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.

29 Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m'banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ace, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? ndipo pamenepo adzafunkha za m'banja lace.

30 Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.

31 Cifukwa cace ndinena kwa inu, Macimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma camwano ca pa Mzimu Woyera sicidzakhululukidwa.

32 Ndipo amene ali yense anganenere Mwana wa munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene ali yense anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi yino kapena irinkudzayo.

Mitengo ndi zipatso zao

33 Ukakoma mtengo, cipatso cace comwe cikoma; ukaipa mtengo, cipatso cace comwe ciipa; pakuti ndi cipatso cace mtengo udziwika.

34 Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwace kwa mtima.

35 Munthu wabwino aturutsa zabwino m'cuma cace cabwino, ndi munthu woipa aturutsa zoipa m'cuma cace coipa.

36 Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pace, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wace tsiku la kuweruza.

37 Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.

Cizindikilo ca Yona

38 Pomwepo alembi ndi Afarisi ena anayankha Iye nati, Mphunzitsi, tifuna kuona cizindikiro ca Inu.

39 Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Akubadwa oipa acigololo afunafuna cizindikiro; ndipo sicidzapatsidwa kwa iwo cizindikiro, komatu cizindikiro ca Yona mneneri;

40 pakuti monga Yona anali m'mimba mwa cinsomba masiku atatu ndi usiku wace, comweco Mwana wa munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wace.

41 1 Anthu a ku Nineve adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; cifukwa 2 iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwace kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Y ona ali pano.

42 3 Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; cifukwa iye anacokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomo; ndipo onani, wakuposa Solomo ali pano.

43 Koma mzimu wonyansa, utaturuka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza.

44 Pomwepo unena, ndidzabwerera kunka kunyumba kwanga, konkuja ndinaturukako; ndipo pakufikako uipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa.

45 Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu yina inzace isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo 4 matsirizidwe ace a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ace. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.

Abale a Yesu

46 Pamene Iye anali cilankhulire ndi makamu, onani, amace ndi 5 abale ace anaima panja, nafuna kulankhula naye.

47 Ndipo munthu anati kwa Iye, Onani, amai wanu ndi abale anu aima pabwalo, nafuna kulankhula nanu.

48 Koma Iye anayankha, nati kwa iye wonenayo, Amai wanga ndani? ndi abale anga ndi ayani?

49 Ndipo anatambalitsa dzanja lace pa ophunzira ace, nati, Penyani amai wanga ndi abale anga!

50 Pakuti 6 ali yense amene adzacita cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28