1 Ndipo pakutsika pace paphiripo, inamtsata mipingo yambiri ya anthu.
2 Ndipo onani, wakhate anadza namgwadira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza.
3 Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lace, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lace linacoka.
4 Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwaiwo.
5 Ndipo m'mene Iye analowa m'Kapernao anadza kwa Iye kenturiyo, nampemba Iye,
6 nati, Ambuye, mnyamata wanga ali gone m'nyumba wodwala manjenje, wozunzidwa koopsa,
7 Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamciritsa iye.
8 Koma kenturiyoyo anabvomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa chindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzaciritsidwa mnyamata wanga.
9 Pakuti inenso ndiri munthu wakumvera ulamuliro, ndiri nao asilikari akundimvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndi kwa kapolo wanga, Cita ici, nacita.
10 Ndipo pakumva ici, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israyeli, sindinapeza cikhulupiriro cotere.
11 Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba;
12 koma anawo a Ufumu adzatayidwa ku mdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
13 Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anaciritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo.
14 Ndipo pofika Yesu ku nyumba ya Petro, anaona mpongozi wace ali gone, alikudwala malungo.
15 Ndipo anamkhudza dzanja lace, ndipo malungo anamleka mkaziyo; ndipo anauka, namtumikira Iye.
16 Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi mizimu yoipa; ndipo Iye anaturutsa mizimuyo ndi mau, naciritsa akudwala onse;
17 kotero kuti cikwaniridwe conenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti,Iye yekha anatenga zofoka zathu,Nanyamula nthenda zathu.
18 Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamulira ophunzira amuke ku tsidya lina,
19 Ndipo anadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kuli konse mumukako.
20 Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wace.
21 Ndipo wina wa ophunzira ace anati kwa Iye, Ambuye, mundilole ine nditange ndamuka kuika maliro a atate wanga.
22 Koma Yesu ananena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa aike akufa ao.
23 Ndipo pamene Iye atalowa m'ngalawa, ophunzira ace anamtsata Iye.
24 Ndipo onani, m panauka namondwe wamkuru panyanja, kotero kuti ngalawa inapfundidwa ndi mafunde: koma Iye anali m'tulo.
25 Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tirikutayika.
26 Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikuru.
27 Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
28 Ndipo pofika Iye ku tsidya lina, ku dziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akuturuka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapa munthu pa njira imeneyo.
29 Ndipo onani, anapfuula nati, Tiri nanu ciani, inu Mwana wa Mulungu? mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yace siinafike?
30 Ndipo panali patari ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zirinkudya.
31 Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutiturutsa, mutitumize ife tilowe m'gulu la nkhumbazo.
32 Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inaturuka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi.
33 Koma akuziweta anathawa, namuka kumidzi, nauza zonse, ndi zakuti zao za aziwanda aja.
34 Ndipo onani, mudzi wonse unaturukira kukakumana naye Yesu, ndipo m'mene anamuona Iye, anampempha kuti acoke m'malire ao.