Mateyu 27 BL92

Yudase adzipacika yekha

1 Ndipo pakudza mamawa, ansembe akuru ndi akuru a anthu onse anakhala upo wakumcitira Yesu, kuti amuphe;

2 ndipo anammanga Iye, namuka naye, nampereka Iye kwa Pilato kazembeyo.

3 Pamenepo Yudase yemwe anampereka Iye, poona kuti Iye anatsutsidwa kuti afe, analapa, nabweza ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe akuru ndi akuru,

4 nanena, Ndinacita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tiri naco ciani ife? udzionere wekha.

5 Ndipo iye anataya pansi ndalamazo paKacisi, nacokapo, nadzipacika yekha pakhosi.

6 Ndipo ansembe akuru anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'cosonkhera ndalama za Mulungu, cifukwa ndizo mtengo wa mwazi.

7 Koma anapangana, nazigula munda wa woumba mbiya, ukhale manda a alendo.

8 Cifukwa cace munda umenewu anaucha, Munda-wa-mwazi, kufikira lero lino.

9 Pamenepo cinakwaniridwa conenedwa ndi Yeremiya mneneri, ndi kuti,Ndipo iwo anatenga ndalamazo zasiliva makumi atatu,Mtengo wa uja wowerengedwa mtengo wace,Amene iwo a ana a Israyeli anawerenga mtengo wace;

10 Ndipo anazipereka kugula munda wa woumba mbiya,Monga anandilamulira ine Ambuye.

Yesu kwa Pilato

11 Ndipo Yesu anaimirira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo anamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero.

12 Ndipo pakumnenera Iye ansembe akuru ndi akuru, Iye sanayankha kanthu.

13 Pomwepo Pilato ananena kwa Iye, Sukumva kodi zinthu zambiri zotere akunenera Iwe?

14 Ndipo sanayankha Iye, ngakhale mau amodzi, kotero kuti kazembe anazizwa ndithu.

15 Ndipo pa Paskha kazembe adazolowera kumasulira anthu mmodzi wandende, amene iwo anafuna.

16 Ndipo pa nthawi yomweyo anali ndi wandende wodziwika, dzina lace Baraba.

17 Cifukwa cace pamene anasonkhana, Pilato ananena kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Baraba kodi, kapena Yesu, wochedwa Kristu?

18 Pakuti anadziwa kuti anampereka Iye mwanjiru.

19 Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wace anatumiza mau kwa iye, kunena, Musacite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri cifukwa ca Iye.

20 Koma ansembe akuru anapangira anthu kuti apemphe Baraba, koma kuti aononge Yesu.

21 Koma kazembe anati kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awa awiri? Ndipo iwo anati, Baraba.

22 Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzacita ciani ndi Yesu, wochedwa Kristu?

23 Onse anati, Apacikidwe pamtanda. Ndipo iye anati, Cifukwa ninji? anacita coipa cotani? Koma iwo anapfuulitsa kopambana, Apacikidwe pamtanda.

24 Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndiribe kucimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.

25 Ndipo anthu onse anabvomereza, ndi kuti, Mwazi wace uli pa ife ndi pa ana athu.

26 Pomwepo iye anamasulira iwo Baraba, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampacike pamtanda.

27 Pomwepo asilikari a kazembe anamuka naye Yesu ku bwalo la mirandu, nasonkhanitsa kwa iye khamu lao lonse.

28 Ndipo anabvula malaya ace, nambveka malaya ofiira acifumu.

29 Ndipo analuka korona waminga, nambveka pamutu pace, namgwiritsa bango m'dzanja lamanja lace; ndipo anagwada pansi pamaso pace, namcitira cipongwe, nati, Tikuoneni, Mfumu ya Ayuda!

30 Namthira malobvu, natenga bango, nampanda Iye pamutu.

31 Ndipo pamene anatha kumcitira Iye cipongwe, anabvula malaya aja, nambveka Iye malaya ace, namtsogoza Iye kukampacika pamtanda.

Ampacika Yesu

32 Ndipo pakuturukapao anapeza munthu wa ku Kurene, dzina lace Simoni, namkangamiza iye kuti anyamule mtanda wace.

33 Ndipo pamene anadza kumalo dzina lace Golgota, ndiko kunena kuti, Malo-abade,

34 anamwetsa Iye vinyo wosanganiza ndi ndulu; ndipo Iye, m'mene analawa, sanafuna kumwa.

35 Ndipo pamene anampacika Iye, anagawana zobvala zace ndi kulota maere:

36 nakhala iwo pansi, namdikira kumeneko.

37 Ndipo anaika pamwamba pamutu pace liwongo lace lolembedwa: UYU NDI YESU MFUMU YA AYUDA.

38 Pamenepo anapacika pamodzi ndi Iyeacifwamba awiri, mmodzi ku dzanja lamanja, ndi wina kulamanzere.

39 Ndipo anthu akupitirirapo 1 anamcitira mwano Iye ndi kupukusa mitu yao,

40 nati, Nanga 2 Iwe, wopasula Kacisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; 3 ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo.

41 Comweconso ansembe akuru, pamodzi ndi alembi ndi akuru anamcitira cipongwe, nati,

42 Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye Mfumu ya Ayuda; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye.

43 4 Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.

44 Ndiponso 5 acifwambawo opacikidwa pamodzi ndi Iye, anamlalatira Iye mau amodzimodzi.

45 Ndipo 6 ora lacisanu ndi cimodzi panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lacisanu ndi cinai.

46 Ndipo poyandikira ora lacisanu ndi cinai, Yesu 7 anapfuula ndi mau akuru, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?

47 Ndipo ena a iwo akuimirira komweko, pamene anamva, ananena, Uyo aitana Eliya.

48 Ndipo pomwepa mmodzi wa iwo anathamanga, 8 natenga cinkhupule, nacidzaza ndi vinyo wosasa, naciika pabango, namwetsa Iye.

49 Koma ena anati, Taleka, tione ngati Eliya adzafika kudzampulumutsa.

50 Ndipo Yesu, 9 pamene anapfuula ndi mau akuru, anapereka mzimu wace.

51 Ndipo onani, 10 cinsaru cocinga ca m'Kacisi cinang'ambika pakati, kucokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika;

52 ndi Manda anatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka;

53 ndipo anaturuka m'manda mwao pambuyo pa kuuka kwace, nalowa m'mzinda woyera, naonekera kwa anthu ambiri.

54 Ndipo pamene mkuru wa asilikari, ndi iwo anali naye 11 akudikira Yesu, anaona cibvomezi, ndi zinthu zimene zinacitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyo ndiye Mwana wa Mulungu.

55 Ndipo anali pomwepo akazi ambiri, akuyang'anira patari, 12 Omwe anatsata Yesu kucokera ku Galileya, namatumikira Iye;

56 mwa iwo 13 amene munali Mariya wa Magadala, ndi Mariya amace wa Yakobo, ndi wa Yose, ndi amace wa ana a Zebedayo.

Amuika Yesu kumanda

57 Ndipo pamene panali madzulo, anadza munthu wacuma wa ku Arimateya, dzina lace Yosefe, amene analinso wophunzira wa Yesu;

58 yemweyo anapita kwa Pilato, napempha mtembo wa Yesu. Pomwepo Pilato analamula kuti uperekedwe.

59 Ndipo Yosefe anatenga mtembo, naukulunga m'nsaru yabafuta yoyeretsa,

60 14 nauika m'manda ace atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukuru pakhomo pa manda, nacokapo,

61 Ndipo Mariya wa Magadala anali pamenepo, ndi Mariya winayo, anakhala pansi popenyana ndi mandawoo

62 Ndipo m'mawa mwace, ndilo dzuwa lotsatana ndi tsiku lokonzera, ansembe akuru ndi Afarisi anasonkhanira kwa Pilato,

63 nanena, Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, 15 Ndidzaukapofikamasikuatatu.

64 Cifukwa cace mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lacitatulo, kuti kapena ophunzira ace angadze, nadzamuba Iye, nadzanena kwa anthu, kuti Iye anauka kwa akufa: ndipo cinyengo comariza cidzaposa coyambaco.

65 Pilato anati kwa iwo, Tengani alonda; mukani, kasungeni monga mudziwa.

66 Ndipo iwo anamuka, nasunga manda, 16 nasindikizapo cizindikiro pamwalapo, iwo pamodzi ndi alondawo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28