1 Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ace khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuiturutsa, ndi yakuciza nthenda iri yonse ndi zofoka zonse.
2 Ndipo maina ao a atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa: woyamba Simoni wochedwa Petro, ndi Andreya mbale wace; Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace;
3 Filipo, ndi Bartolomeyo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkhoyo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
4 Simoni Mkanani, ndi Yudasi Isikariote amenenso anampereka Iye.
5 Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti,Musapite ku njira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:
6 koma makamaka mupite ku nkhosa zosokera za banja la Israyeli.
7 Ndipo pamene mulikupita lalikani kuti, Ufumu wa Kumwamba wayandikira.
8 Ciritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, turutsani ziwanda: munalandira kwaulere, patsani kwaulere.
9 Musadzitengere ndalama zagolidi, kapena zasiliva, kapena zakobiri m'malamba mwanu;
10 kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wanchito ayenera kulandira zakudya zace.
11 Ndipo m'mzinda uliwonse, kapena m'mudzi mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira muturukamo.
12 Ndipo polowa m'nyumba muwalankhule.
13 Ndipo ngati nyumbayo iri yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siiri yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.
14 Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mau anu, pamene mulikuturuka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani pfumbi m'mapazi anu.
15 Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodomu ndi Gomora udzacepa ndi wace wa mudzi umenewo.
16 Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa afisi; cifukwa cace khalani ocenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
17 Koma cenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akuru a mlandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;
18 Ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu cifukwa ca Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.
19 Koma pamene pali ponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene ciani; pakuti cimene mudzacilankhula, cidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo;
20 pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.
21 Ndipo mbale adzapereka mbale wace kuimfa, ndi atate mwana wace: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.
22 Ndipo adzada inu anthu onse cifukwa ca dzina langa; koma iye wakupirira kufikira cimariziro, iyeyu adzapulumutsidwa.
23 Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israyeli, kufikira Mwana wa munthu atadza.
24 Wophunzira saposa mphunzitsi wace, kapena kapolo saposa mbuye wace.
25 Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wace, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamucha mwini banja Beelzebule, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ace?
26 Cifukwa cace musaopa iwo; pakuti palibe kanthu kanabvundikiridwa, kamene sikadzaululidwa; kapena kanthu kobisika, kamene sikadzadziwika.
27 Cimene ndikuuzani inu mumdima, tacinenani poyera; ndi cimene mucimva m'khutu, mucilalikire pa macindwi nyumba.
28 Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe m'gehena.
29 Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu:
30 komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa.
31 Cifukwa cace musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.
32 Cifukwa cace yense amene adzabvomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso nelidzambvomereza iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.
33 Koma 1 yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso nelidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.
34 2 Musalingalire kuti nelidadzera kuponya mtendere pa dziko lapansi; sinelinadzera kuponya mtendere, koma lupanga.
35 3 Pakuti ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate wace, ndi mwana wamkazi ndi amace, ndi mkazi wokwatiwa ndi mpongozi wace:
36 ndipo 4 apabanja ace a munthu adzakhala adani ace.
37 5 Iye wakukonda atate wace, kapena amace koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wace wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.
38 Ndipo 6 iye amene satenga mtanda wace, natsata pambuyo panga, sayenera Ine.
39 7 Iye amene apeza moyo wace, adzautaya; ndi iye amene ataya moyo wace, cifukwa ca Ine, adzaupeza.
40 8 Iye wakulandira inu, andilandira Ine, ndi wakundilandira Ine, amlandira Iye amene ananditumiza Ine.
41 9 Iye wakulandira mneneri, pa dzina la mneneri, adzalandira mphotho ya mneneri; ndipo wakulandira munthu wolungama, pa dzina la munthu wolungama, adzalandira mphotho ya munthu wolungama.
42 Ndipo 10 amenealiyense adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa cikho cokha ca madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yace.