1 Nthawi yomweyo ophunzira anadza kwa Yesu, nanena, Ndani kodi ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba?
2 Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao,
3 nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.
4 Cifukwa cace yense amene adzicepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.
5 Ndipo amene adzalandira kamwana kamodzi kotereka cifukwa ca dzina langa, alandira Ine;
6 koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikuru ikolowekedwe m'khosi mwace, namizidwe poya pa nyanja.
7 Tsoka liri hdi dziko lapansi cifukwa ca zokhumudwitsa! pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka liri ndi munthu amene cokhumudwitsaco cidza ndi iye.
8 Ndipo ngati dzanja lako, kapena phazi lako likukhumudwitsa iwe, ulidule, nulitaye; nkwabwino, kuti ulowe m'moyo wopunduka dzanja kapena phazi, koposa kuponyedwa m'moto wa nthawi zonse, uli ndi manja awiri kapena mapazi awiri.
9 Ndipo ngati diso lako likukhumudwitsa, ulikolowole, nulitaye: nkwabwino kuti ulowe m'moyo ndi diso limodzi koposa kuponyedwa m'gehena wamoto, uli ndi maso awiri.
10 Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya cipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba. [
11 ]
12 Nanga muyesa bwanji? ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo ikasokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anai mphambu manu ndi zinai, napita kumapiri, kukafuna yosokerayo?
13 Ndimo akaipeza, indedi ndinena kwa inu, akondwera nayo koposa ndi makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai zosasokera.
14 Comweco siciri cifuniro ca Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang'ono awa atayike.
15 Ndipo ngati mbale wako akucimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.
16 Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.
17 Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.
18 Indetu ndinena kwa inu, Ziri zonse mukazimanga pa dziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo ziri zonse mukazimasula pa dziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba.
19 Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri ainu abvomerezana pansi pano cinthu ciri conse akacipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawacitira.
20 Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndiri komweko pakati pao.
21 Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? kufikira kasanu ndi kawiri kodi?
22 Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi ananu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.
23 Cifukwa cace Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, mfumu, amene anafuna kuwerengera nao akapolo ace.
24 Ndipo pamene anayamba kuwerengera, anadza kwa iye ndi wina wamangawa wa ndalama za matalente zikwi khumi.
25 Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wace analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wace ndi ana ace omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo.
26 Cifukwa cace kapoloyo anagwadapansi, nampembedzera, nati, Mbuye, bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzazibwezera kwa inu.
27 Ndipo mbuye wa kapoloyo anagwidwa ndi cisoni mumtima, nammasula iye, namkhululukira ngongole.
28 Koma kapolo uyu, poturuka anapeza wina wa akapolo anzace yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera cija unacikongola.
29 Pamenepo kapolo mnzaceyu anagwada pansi, nampempha iye, nati, Bakandiyembekeza ine, ndipo ndidzakubwezera.
30 Ndipo iye sanafuna; koma anamuka, namponya iye m'nyumba yandende, kufikira abwezere ngongole.
31 Cifukwa cace m'mene akapolo anzace anaona zocitidwazo, anagwidwa cisoni cacikuru, nadza, nalongosolera mbuye wao zonse zimene zinacitidwa.
32 Pomwepo mbuye wace anamuitana iye, nanena naye, Kapolo iwe weipa, ndinakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja unandipempha ine;
33 kodi iwenso sukadamcitira kapolo mnzako cisoni, monga inenso ndinakucitira iwe cisoni?
34 Ndipo mbuye wace anakwiya, nampereka kwa azunzi, kufikira akambwezere iye mangawa onse.
35 Comweconso Atate wanga adzacitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wace ndi mitima yanu.