1 Ndipo Afarisi ndi Asaduki anadza, namuyesa, namfunsa Iye awaonetse cizindikiro ca Kumwamba.
2 Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Madzulo munena, Kudzakhala ngwe; popeza thambo liri laceza.
3 Ndipo m'mawa, Lero nkwa mphepo; popeza thambo liri la ceza codera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo yin o, simungathe kuzindikira.
4 Obadwa oipa ndi acigololo afunafuna cizindikiro; ndipo sadzalandira cizindikiro cina, koma cizindikiro ca Yona. Ndipo Iye anawasiya, nacokapo.
5 Ndipo ophunzira anadza ku tsidya linalo, naiwala kutenga mikate.
6 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Yang'anirani mupewe cotupitsa mkate ca Afarisi ndi Asaduki.
7 Ndipo iwo anafunsana wina ndi mnzace, nati, Sitinatenga mikate.
8 Koma Yesu, m'mene anadziwa, anati, Ha, inu okhulupirira pang'ono, mufunsana cifukwa ninji wina ndi mnzace, kuti simunatenga mikate?
9 kodi cikhalire simudziwa, ndipo simukumbukira mikate isanu ija ya anthu aja zikwi zisanu, ndi mitanga ingati munaitola?
10 Penanso mikate isanu ndi iwiri ija ya anthu zikwi zinai, ndi malicero angati munawatola?
11 Bwanji nanga simudziwa kuti sindinanena kwa inu za mikate? Koma pewani cotupitsa ca Afarisi ndi Asaduki.
12 Pomwepo anadziwitsa kuti sanawauza kupewa cotupitsa ca mikate, koma ciphunzitso ca Afarisi ndi Asaduki.
13 Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kaisareya wa Filipi, anafunsa ophunzira ace, kuti, Anthu anena kuti Mwana wa munthu ndiye yani?
14 Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.
15 Iye ananena kwa iwo, Koma inu mutani kuti Ine ndine yani?
16 Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.
17 Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bar-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululira ici, koma Atate wanga wa Kumwamba.
18 Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzaulaka uwo.
19 Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo cimene ukamanga pa dziko lapansi cidzakhala comangidwa Kumwamba: ndipo cimene ukacimasula pa dziko lapansi, cidzakhala comasulidwa Kumwamba.
20 Pamenepo analamulira ophunzira kuti asauze munthu kuti Iye ndiye Kristu.
21 Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ace, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akuru, ndi ansembe akuru, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lacitatu kuuka kwa akufa.
22 Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula, kuti, Dzicitireni cifundo, Ambuye; sicidzatero kwa Inu ai.
23 Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe condikhumudwitsa Ine; cifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.
24 Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ace, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wace, nanditsate Ine.
25 Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wace adzautaya: koma iye amene ataya moyo wace cifukwa ca Ine, adzaupeza.
26 Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wace? kapena munthu adzaperekanji cosintha ndi moyo wace?
27 Pakuti Mwana wa munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wace, pamodzi ndi angelo ace; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga macitidwe ao.
28 Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pane sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa munthu atadza mu ufumu wace.