Mateyu 13 BL92

Fanizo la Wofesa

1 Tsiku lomwelo Yesu anaturuka m'nyumbamo, nakhala pansi m'mbali mwa nyanja.

2 Ndipo makamu ambiri a anthu anasonkhanira kwa Iye, kotero kuti Iye analowa m'ngalawa, nakhala pansi, ndipo khamu lonse linaima pamtunda.

3 Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anaturuka kukafesa mbeu,

4 Ndipo m'kufesa kwace zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nizilusira izo.

5 Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhala nalo dothi lakuya, Ndipo m'mene dzuwa linakwera zinapserera;

6 ndipo popeza zinalibe mizu zinafota.

7 Koma zina zinagwa paminga, ndipo mingayo inayanga, nizitsamwitsa izo.

8 Koma zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu.

9 Amene ali ndi makutu, amve.

10 Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Cifukwa canji muphiphiritsira iwo m'mafanizo?

11 Ndipo Iye anayankha nati, Cifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo.

12 Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zocuruka; koma yense amene alibe, cingakhale comwe ali naco cidzacotsedwa kwa iye.

13 Cifukwa cace ndiphiphiritsira iwo m'mafanizo; cifukwa kuti akuona samaona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa.

14 Ndipo adzacitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati.Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse;Pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse;

15 Cifukwa unalemera mtima wa anthuawa,Ndipo m'makutu ao anamva mogontha,Ndipo maso ao anatsinzina;Kuti asaone konse ndi maso,Asamve ndi makutu,Asazindikire ndi mtima wao,Asatembenuke,Ndipo ndisawaciritse iwo.

16 Koma maso anu ali odala, cifukwa apenya; ndi makutu anu cifukwa amva.

17 Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama analakalaka kupenya zimene muziona, koma sanaziona; ndi kumva zimene muzimva, koma sanazimva.

Kumasulira kwa fanizo la wofesa

18 Ndipo tsono mverani inu fanizolo la wofesa mbeu uja.

19 Munthu ali yense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula cofesedwaco mumtima mwace. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.

20 Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mau, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera;

21 ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo cifukwa ca mau, iye akhumudwa pomwepo.

22 Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi cinyengo ca cuma citsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda cipatso.

23 Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.

Fanizo la namsongole

24 Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwace;

25 koma m'mene anthu analinkugona, mdani wace anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nacokapo.

26 Koma pamene mmera unakula, nubala cipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole.

27 Ndipo anyamata ace a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? nanga wacokera kuti namsongoleyo?

28 Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wacicita ici. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse uyo pamodzi?

29 Koma iye anati, lai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye.

30 Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.

Fanizo la kambeu kampiru ndi la cotupitsa mkate

31 Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi kambeu kampiru, kamene anakatenga munthu, nakafesa pamunda pace;

32 kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakuru kuposa zitsambazonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nizibindikira mu nthambi zace.

33 Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi cotupitsa mikate, cimene mkazi anacitenga, nacibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.

34 Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhula kanthu kwa iwo;

35 kuti cikacitidwe conenedwa ndi mneneri, kuti,Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo;Ndidzaulula zinthu zobisika ciyambire kukhazikidwa kwace kwa dziko lapansi.

Yesu awatanthauzira fanizo la namsongole

36 Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ace anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.

37 Ndipo Iye anayankha nati, Wofesa mbeu yabwino ndiye Mwana wa munthu;

38 ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo;

39 ndipo mdani amene anamfesa uwu ndiye mdierekezi: ndi kututa ndico cimariziro ca nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo.

40 Ndipo monga namsongole asonkhanitsidwa pamodzi, natenthedwa pamoto, matero mudzakhala m'cimariziro ca nthawi ya pansi pano.

41 Mwana wa munthu adzatuma angelo ace, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kucotsa mu Ufumu wace zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akucita kusayeruzika,

42 ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

43 Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve.

Fanizo la cuma cobisika, la ngale la khoka

44 Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi cuma cobisika m'munda; cimene munthu anacipeza, nacibisa; ndipo m'kucikonda kwace acoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.

45 Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino:

46 ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatari, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.

47 Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m'nyanja, ndi 1 kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse;

48 limene podzala, analibvuulira pamtunda; ndipo m'mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m'zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo.

49 Padzatero pa cimariziro ca nthawi ya pansi pano: angelo adzaturuka, 2 nadzawasankhula oipa pakati pa abwino,

50 nadzawataya m'ng'anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

51 Mwamvetsa zonsezi kodi? lwo anati kwa Iye, inde.

52 Ndipo Iye anati kwa iwo, Cifukwa cace, mlembi ali yense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene aturutsa m'cuma cace zinthu zakale ndi zatsopano.

Ampeputsa Yesu ku Nazarete

53 Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anacokera kumeneko.

54 Ndipo 3 pofika ku dziko la kwao, anaphunzitsa iwo m'sunagoge mwao, kotero kuti anazizwa, nanena, Uyu adazitengakuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu izi?

55 4 Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? kodi dzina lace la amace si Mariya? ndi 5 abale ace si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda?

56 Ndipo alongo ace sali ndife onsewa? Ndipo iyeyo adazitenga zinthu zonsezi kuti?

57 Ndipo iwo anakhumudwa cifukwa ca Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, 6 Mneneri sakhala wopanda ulemu koma ku dziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwace.

58 Ndipo Iye, cifukwa ca kusakhulupirira kwao, sanacita kumeneko zamphamvu zambiri.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28