Mateyu 23 BL92

Yesu adzudzula Alembi ndi Afarisi

1 Pomwepo Yesu analankhula ndi makamu a anthu ndi ophunzira ace,

2 nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose;

3 cifukwa cace zinthu ziri zonse zimene iwo akauza inu, citani nimusunge; koma musatsanza nchito zao; pakuti iwo amalankhula, komasamacita.

4 Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi cala cao.

5 Koma amacita nchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa citando cace ca njirisi zao, nakulitsa mphonje,

6 nakonda malo a ulemu pamapwando, ndi mipando ya ulemu m'masunagoge,

7 ndi kulankhulidwa m'misika, ndi kuchedwa ndi anthu, Rabi.

8 Koma inu musachedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.

9 Ndipo inu musachule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba.

10 Ndipo musachedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.

11 Koma wamkuru wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu.

12 Ndipo amene ali yense akadzikuza yekha adzacepetsedwa; koma amene adzicepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.

13 Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, Ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo. [

14 ]

15 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m'mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa gehena woposa inu kawiri.

16 Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene ali yense akalumbira kuchula Kacisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kuchula golidi wa Kacisi, wadzimangirira.

17 Inu opusa, ndi akhungu: pakuti coposa nciti, golidi kodi, kapena Kacisi amene ayeretsa golidiyo?

18 Ndiponso, Amene ali yense akalumbira kuchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kuchula mtulo wa pamwamba pace wadzimangirira.

19 Inu akhungu, pakuti coposa nciti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?

20 Cifukwa cace wakulumbira kuchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pace.

21 Ndipo wakulumbira kuchula Kacisi, alumbira ameneyo ndi Iye wakukhala momwemo.

22 Ndipo wakulumbira kuchula Kumwamba, alumbira cimpando ca Mulungu, ndi Iye wakukhala pomwepo.

23 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la citowe, nimusiya zolemera za cilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kucitira cifundo, ndi cikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzicita, osasiya izi zomwe.

24 Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma ngamila mummeza.

25 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mutsuka kunja kwace kwa cikho ndi mbale, koma m'katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa.

26 Mfarisi iwe wakhungu, yambotsuka m'kati mwa cikho ndi mbale, kuti kunja kwace kukhalenso koyera.

27 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwace, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.

28 Comweco inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi cinyengo ndi kusayeruzika.

29 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mumanga nyumba za pa manda a aneneri, ndipo mukonza manda a anthu olungama,

30 ndi kuti, Ife tikadakhala m'masiku a makolo anthu, sitikadakhala oyanjana nao pa mwazi wa aneneri.

31 Pomwepo mutsimikiza nokha, kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri.

32 Dzazani inu muyeso wa makolo anu.

33 Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthawa kulanga kwace kwa gehena?

34 Cifukwa ca ici, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapacika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m'masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kucokera ku mudzi umodzi, kufikira ku mudzi wina;

35 kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa pa dziko lapansi, kuyambira ku mwazi wa Abele wolungamayo, kufikira ku mwazi wa Zakariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Kacisi ndi guwa la nsembe.

36 Indetu ndinena kwa inu, Zinthu zonse izi zidzafika pa mbadwo uwu wamakono.

37 Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ace m'mapiko ace, koma inu simunafuna ai!

38 Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.

39 Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandionanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena,Wolemekezedwa Iye amene akudza m'dzina la Ambuye.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28