Mateyu 14 BL92

Herode amupha Yohane Mbatizi

1 Nthawi imeneyo Herode mfumu anamva mbiri ya Yesu,

2 nanena kwa anyamata ace, U yo ndiye Yohane Mbatizi; anauka kwa akufa; ndipo cifukwa ca ici zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye.

3 Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende cifukwa ca Herodiya, mkazi wa mbale wace Filipo.

4 Pakuti Yohane ananena kwa iye, Sikuloledwa kwa iwe kukhala naye.

5 Ndipo pofuna kumupha iye, anaopa khamu la anthu, popeza anamuyesa iye mneneri.

6 Koma pakufika tsiku la kubadwa kwace kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiya anabvina pakati pao, namkondweretsa Herode.

7 Pomwepo iye anamlonjeza cilumbirire, kumpatsa iye cimene ciri conse akapempha.

8 Ndipo iye, atampangira amace, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbizi mutu wa Yohane Mbatizi. Ndipo mfumuyo anagwidwa ndi cisoni;

9 koma cifukwa ca malumbiro ace, ndi ca iwo anali naye pacakudya, analamulira upatsidwe;

10 ndipo anatumiza mnyamata, namdula mutu Yohane m'nyumba yandende.

11 Ndipo anautenga mutu wace m'mbizimo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amace.

12 Ndipo ophunzira ace anadza, natola mtembo, nauika; ndipo anadza nauza Yesu.

Yesu acurukitsa mikate poyamba paja

13 Ndipo Yesu pakumva, anacokera kumeneko m'ngalawa, kunka ku malo acipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kucokera m'midzi.

14 Ndipo Iye anaturuka, naona khamu lalikuru la anthu, nacitira iwo cifundo, naciritsa akudwala ao.

15 Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ace anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga cipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite ku midzi kukadzigulira okha kamba.

16 Koma Yesu anati kwa iwo, Iwo alibe cifukwa ca kumukira, apatseni ndinu adye.

17 Koma iwo ananena kwa Iye, Ife tiribe kanthu pano koma mikate isanu, ndi nsomba ziwiri.

18 Ndipo Iye anati, Mudze nazo kuno kwa Ine.

19 Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi pamaudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.

20 Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, mitanga khumi ndi iwiri yodzala.

21 Ndipo anadyawo anali amuna monga zikwi zisanu, kuwaleka akazi ndi ana.

Yesu ayenda panyanja

22 Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera Iye ku tsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke.

23 Ndipo pamene Iye anawauza makamuwo, anakwera m'phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha.

24 Koma pomwepo ngalawa idafika pakati pa nyanja, yozunzika ndi mafunde; pakuti mphepo inadza mokomana nao.

25 Ndipo pa ulonda wacinai wa usiku, Iye anadza kwa iwo, nayenda pamwamba pa nyanja.

26 Koma m'mene ophunzirawo anamuona Iye, alikuyenda pamadzi, ananthunthumira, nati, ndi mzukwa! Ndipo anapfuula ndi mantha.

27 Koma pomwepo Yesu analankhula nao, nati, Limbani mtima; ndine; musaope.

28 Ndipo Petro anamyankha Iye nati, Ambuye, ngati ndinutu, mundiuze ndidze kwa lou pamadzi.

29 Ndipo Iye anati, Idza, Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.

30 Koma m'mene iye anaiona mphepo, ana, opa; ndipo poyamba kunura, anapfuula, nati, Ambuye, ndipulumutseni ine!

31 Ndipo pomwepo Yesu anatansa dzanja lace, namgwira iye, nanena naye, Iwe wokhulupirira pang'ono, wakayikiranji mtima?

32 Ndipo pamene iwo analowa m'ngalawamo, mphepo inaleka.

33 Ndipo iwo amene anali m'ngalawamo anamgwadira, nanena, Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.

34 Ndipo pamene iwo anaoloka, anafika kumtunda, ku Genesarete.

35 Ndipo m'meneamuna a pamenepo anamzindikira, anatumiza konse ku dziko lonse lozungulira, nadzanao kwa Iye onse akukhala ndi nthenda;

36 ndipo anampempha Iye, kuti akhudze yokha mphonje ya cobvala cace; ndipo onse amene anamkhudza anaciritsidwa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28