1 Ndipo panali pamene Yesu anatha mau amenewa, anacokera ku Galileya, nadza ku malire a Yudeya, a ku tsidya lija la Yordano.
2 Ndipo makamu akuru a anthu anamtsata; ndipo Iye anawaciritsa kumeneko.
3 Ndipo Afarisi anadza kwa Iye, namuyesa, nanena, Kodi nkuloledwa kuti munthu acotse mkazi wace pa cifukwa ciri conse?
4 Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu paciyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi,
5 nati, Cifukwa ca ici mwamuna adzasiya atate wace ndi amace, nadzaphatikizana ndi mkazi wace, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi?
6 cotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Cifukwa cace ici cimene Mulungu anacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.
7 Iwo ananena kwa Iye, Nanga cifukwa ninji Mose analamulira kupatsa kalata wa cilekaniro, ndi kumcotsa?
8 Iye ananena kwa iwo, Cifukwa ca kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kucotsa akazi anu; koma paciyambi sikunakhala comweco.
9 Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene ali yense akacotsa mkazi wace, kosakhala cifukwa ca cigololo, nadzakwatira wina, acita cigololo: ndipo iye amene akwatira wocotsedwayo, acita cigololo.
10 Ophunzira ananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wace uti wotere, sikuli kwabwino kukwatira.
11 Koma Iye anati kwa iwo, Onse sangathe kulandira conena ici, koma kwa iwo omwe capatsidwa.
12 Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m'mimba ya amao: ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha, cifukwa ca Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ici acilandire.
13 Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ace pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula.
14 Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: cifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.
15 Ndipo Iye anaika manja ace pa ito, nacokapo.
16 Ndipo onani, munthu anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, cabwino nciti ndicicite, kuti ndikhale nao mayo wosatha?
17 Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za cinthu cabwino? alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.
18 Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usacite cigololo, Usabe, Usacite umboni wonama,
19 Lemekeza atate wako ndi amako, ndipo, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.
20 Mnyamatayo ananena kwa Iye, Zonsezi ndinazisunga, ndisowanso ciani?
21 Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhaia ndi cuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.
22 Koma mnyamatayo m'mene anamva conenaco, anamuka wacisoni; pakuti anali naco cuma cambiri.
23 Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ace, Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini cuma adzalowa mobvutika mu Ufumu wa Kumwamba.
24 Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamila ipyole diso la singano, koposa mwini cuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.
25 Ndipo ophunzira, pamene anamva, anazizwa kwambiri, nanena, Ngati nkutero angapulumuke ndani?
26 Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, ici sicitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.
27 Pomwepo Petro anayankha, nati kwa Iye, Onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata Inu; nanga tsono tidzakhala ndi ciani?
28 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa munthu adzakhala pa cimpando ca ulemerero wace, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.
29 Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, cifukwa ca dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.
30 Koma ambiri oyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.