1 Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, naturuka kukakomana ndi mkwati.
2 Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ocenjera.
3 Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengeranso mafuta;
4 koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao.
5 Ndipo pamene mkwati anacedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo.
6 Koma pakati pa usiku panali kupfuula, Onani, mkwati! turukani kukakomana naye.
7 Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zao.
8 Ndipo opusa anati kwa ocenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; cifukwa nyali zathu zirikuzima.
9 Koma ocenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.
10 Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo, analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.
11 Koma pambuyo pace anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife.
12 Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziwani.
13 Cifukwa cace dikirani, pakuti simudziwa tsiku lace, kapena nthawi yace.
14 Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ace, napereka kwa iwo cuma cace.
15 Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye.
16 Pomwepo uyo amene analandira ndalama zisanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo ndalama zina zisanu.
17 Cimodzimodzinso uyo wa ziwirizo, anapindulapo zina ziwiri.
18 Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, naibisa ndalama ya mbuye wace.
19 Ndipo Itapita nthawi yaikuru, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi.
20 Ndipo uyo amene adalandira ndalama za matalente zisanu anadza, ali nazo ndalama zina zisanu, nanena, Mbuye, munandipatsa ndalama za matalente, zisanu, onani ndapindulapo ndalama zisanu zina.
21 Mbuye wace anati kwa iye, Cabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; Iowa iwe m'cikondwero ca mbuye wako.
22 Ndipo wa ndalama ziwiriyo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine ndalama ziwiri; onani, ndapindulapo ndalama zina ziwiri.
23 Mbuye wace anati kwa iye, Cabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; Iowa iwe m'cikondwero ca mbuye wako.
24 Ndipo uyonso amene analandira ndalama imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafesa, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaza;
25 ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi ndalama yanu: onani, siyi yanu.
26 Koma mbuye wace anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafesa, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaza;
27 cifukwa cace ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lace.
28 Cifukwa cace cotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi.
29 Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zocuruka: koma kwa iye amene alibe, kudzacotsedwa, cingakhale cimene anali naco.
30 Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pace ku mdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
31 Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wace, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa cimpando ca kuwala kwace:
32 ndipo adzasonkhanidwa pamaso pace anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzace, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi;
33 nadzakhalitsa nkhosa ku dzanja lace lamanja, koma mbuzi kulamanzere.
34 Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a ku dzanja lace lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa cikhazikiro cace ca dziko lapansi:
35 pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munacereza Ine;
36 wamarisece Ine, ndipo munandibveka; ndinadwala, ndipo munadza kuceza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine.
37 Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? kapena waludzu, ndi kukumwetsani?
38 Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucerezani? kapena wamarisece, ndi kukubvekani?
39 Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu?
40 Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Cifukwa munacitira ici mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandicitira ici Ine.
41 Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a ku dzanja lamanzere, Cokani kwa Ine otembereredwa inu, ku mota wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi amithenga ace:
42 pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatsa Ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetsa Ine:
43 ndinali mlendo, ndipo simunandilandira Ine; wamarisece ndipo simunandibveka Ine; wodwala, ndi m'nyumba yandende, ndipo simunadza kundiona Ine.
44 Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamarisece, kapena m'nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu?
45 Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Cifukwa munalibe kucitira ici mmodzi wa awa ang'onong'ono, munalibe kundicitira ici Ine.
46 Ndipo amenewa adzacoka kumka ku cilango ca nthawi zonse; koma olungama ku moyo wa nthawi zonse.