Marko 14 BL92

Ansembe akulu acita ciwembu pa Yesu

1 Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paskha ndi mikate yopanda cotupitsa; ndipo ansembe akuru ndi alembi anafunafuna momcitira ciwembu, ndi kumupha:

2 pakuti anati, Paphwando ai, kuti pangakhale phokoso la anthu.

Phwando la ku Betaniya

3 Ndipo pakukhala iye ku Betaniya m'nyumba ya Simoni wakhate, m'mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa yaalabastero ya mafuta onunkhira bwino a nardo weni weni a mtengowapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pace.

4 Koma anakhalako ena anabvutika mtima mwa iwo okha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa cifukwa ninji?

5 Pakuti mafuta amene akadagula marupiya atheka mazana atatu ndi mphambu zace, ndi kupatsa aumphawi. Ndipo anadandaulira mkaziyo.

6 Koma Yesu anati, Mlekeni, mumbvutiranji? wandicitira Ine nchito yabwino.

7 Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo pali ponse pamene mukafuna mukhoza kuwacitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.

8 Iye wacita cimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m'manda.

9 Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino ku dziko lonse lapansi, icinso cimene anacita mkazi uyu cidzanenedwa, cikhale comkumbukira naco.

Yudase apangana ndi ansembe akuru

10 Ndipo Yudase Isikariote, ndiye mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anacoka napita kwa ansembe akuru, kuti akampereke Iye kwa iwo.

11 Ndipo pamene iwo anamva, anasekera, nalonjezana naye kuti adzampatsa ndalama. Ndipo iye anafunafuna pompereka Iye bwino.

Paskha wotsiriza, Mgonero wa Ambuye

12 Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda cotupitsa, pamene amapha Paskha, ophunzira ace ananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paskha?

13 Ndipo anatuma awiri a ophunzira ace, nanena nao, Lowani m'mzinda, ndipo adzakomana nanu munthu wakusenza mtsuko wa madzi; mumtsate iye;

14 ndipo kumene akalowako iye, munene naye mwini nyumba, Mphunzitsi anena, Ciri kuti cipinda ca alendo canga, m'menemo ndikadye Paskha ndi ophunzira anga?

15 Ndipo iye yekha adzakusonyezani cipinda ca pamwamba cacikuru coyalamo ndi cokonzedwa; ndipo m'menemo mutikonzere.

16 Ndipo ophunzira anaturuka, nafika m'mzinda, napeza monga anati kwa iwo; ndipo anakonza Paskha.

17 Ndipo pofika madzulo anadza Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.

18 Ndipo pamene anaseama iwo kudya, Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Mmodzi wa inu adzandipereka Ine, ndiye wakudya ndi Ine pamodzi.

19 Anayamba iwo kukhala ndi cisoni, ndi kunena naye mmodzi mmodzi, kuti, Ndine kodi?

20 Ndipo anati kwa iwo, Mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndiye wakusunsa pamodzi ndi Ine m'mbale.

21 Pakuti Mwana wa munthu amukadi, monga kwalembedwa za Iye; koma tsoka munthuyo amene apereka Mwana wa munthu! Kukadakhala bwino kwa munthu ameneyo ngati sakadabadwa iye.

22 Ndipo pamene iwo analikudya, Iye anatenga mkate, ndipo pamene anadalitsa, ananyema, napereka kwa iwo, kuti, Tengani; thupi langa ndi ili.

23 Ndipo anatenga cikho, ndipo pamene adayamika, anapereka kwa iwo; ndipo iwo onse anamweramo.

24 Ndipo Iye anati kwa iwo, ici ndi mwazi wanga wa cipangano, wothiridwa cifukwa ca anthu ambiri.

25 Ndithu ndinena nanu, Sindidzamwanso cipatso ca mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa ico catsopano mu Ufumu wa Mulungu.

26 Ndipo atayimba nyimbo, anaturuka, namuka ku phiri la Azitona.

Yesu acenjeza Petro

27 Ndipo Yesu ananena nao, Mudzakhumudwa nonsenu; pakuti kwalembedwa,Ndidzakantha mbusa, ndi nkhosa zidzamwazika.

28 Komatu nditadzauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.

29 Koma Petro ananena naye, Angakhale adzakhumudwa onse, komatu ine iai.

30 Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.

31 Koma iye analimbitsa mau cilimbitsire, kuti, Ngakhale ndidzafa nanu, sindidzakana Inu. Ndipo onsewo anatero.

Getsemane

32 Ndipo iwo anadza ku malo dzina lace Getsemane; ndipo ananena kwa ophunzira ace, Bakhalani pano, kufikira ndikapemphera.

33 Ndipo anatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kusauka mtima ndithu.

34 Ndipo ananena nao, Moyo wanga uli wa cisoni cambiri, kufikira imfa. Bakhalani pano, nimudikire.

35 Ndipo Iye anapita m'tsogolo pang'ono, nagwa pansi, napemphera kuti ngati nkutheka nthawi imene impitirire.

36 Ndipo ananena, Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundicotsere cikho ici; komatu si cimene ndifuna Ine, koma cimene mufuna Inu.

37 Ndipo anadza nawapeza iwo ali m'tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? unalibe mphamvu yakudikira ora limodzi kodi?

38 Dikirani, pempherani, kuti mungalowe m'kuyesedwa; mzimutu uli wakufuna, koma thupi liri lolefuka.

39 Ndipo anacokanso, napemphera, nanena mau omwewo.

40 Ndipo anadzanso nawapeza ali m'tulo, pakuti maso ao analemeradi; ndipo sanadziwa comyankha Iye.

41 Ndipo anadza kacitatu, nanena nao, Gonani tsopano, nimupumule; cakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa munthu aperekedwa m'manja a anthu ocimwa.

42 Ukani, tizimuka; onani wakundiperekayo ali pafupi.

Amgwira Yesu

43 Ndipo pomwepo, Iye ali cilankhulire, anadza Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nao malupanga ndi mikunkhu, ocokera kwa ansembe akuru ndi alembi ndi akuru.

44 Ndipo wakumpereka Iye anawapatsa cizindikilo, nanena, Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye cisungire.

45 Ndipo atafika, pomwepo anadza kwa Iye, nanena, Rabi; nampsompsonetsa.

46 Ndipo anamthira manja, namgwira.

47 Koma mmodzi wina wa iwo akuimirirapo, anasolola lupanga lace, nakantha kapolo wace wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lace.

48 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi mwaturuka ndi malupanga ndi mikunkhu kundigwira ine monga wacifwamba?

49 Masiku onse ndinali nanu m'Kacisi ndirikuphunzitsa, ndipo simunandigwira Ine; koma ici cacitika kuti malembo akwanitsidwe.

50 Ndipo iwo onse anamsiya Iye, nathawa.

51 Ndipo mnyamata wina anamtsata Iye, atapfundira pathupi bafuta yekha; ndipo anamgwira;

52 koma iye anasiya bafutayo, nathawa wamarisece.

Yesu aweruzidwa ndi akuru a Ayuda

53 Ndipo ananka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo anasonkhana kwa iye ansembe akuru onse ndi akuru a anthu, ndi alembi,

54 Ndipo Petro adamtsata Iye kutali, kufikira kulowa m'bwalo la mkulu wa ansembe; ndipo anali kukhala pansi pamodzi ndi anyamata, ndi kuotha moto.

55 Ndipo ansembe akuru ndi akuru a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeza.

56 Pakuti ambiri anamcitira umboni wonama, ndipo umboni wao sunalingana.

57 Ndipo ananyamukapo ena, namcitira umboni wakunama, nanena kuti,

58 Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kacisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.

59 Ndipo ngakhale momwemo umboni wao sunalingana.

60 Ndipo mkulu wa ansembe ananyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nciani ici cimene awa alikucitira mboni?

61 Koma anakhala cete, osayankhakanthu. Mkulu wa ansembe anamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Kristu, Mwana wace wa Wolemekezeka?

62 Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa munthu alikukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba.

63 Ndipo mkulu wa ansembe anang'amba maraya ace, nanena, Tifuniranjinso mboni zina?

64 Mwamva mwano wace; muyesa bwanji? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti ayenera kufa.

65 Ndipo ena mayamba kumthira malobvu Iye, adi kuphimba nkhope yace, ndi cumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo ananpanda Iye kofu.

Petro akana kuti sadziwa Yesu

66 Ndipo pamene Petro anali iansi m'bwalo, anadzapo mmodzi va adzakazi a mkulu wa ansembe;

67 ndipo anaona Petro alikuotha noto, namyang'ana iye, nanena, wenso unali naye Mnazarene, Yesu.

68 Koma anakana, nanena, Sindidziwa kapena kumvetsa cimene ucinena iwe; ndipo anaturuka kunka kucipata; ndipo tambala analira.

69 Ndipo anamuona mdzakaziyo, nayambanso kunena ndi iwo akuimirirapo, Uyu ngwa awo.

70 Koma anakananso. Ndipo patapita kamphindi, akuimirirapo ananenanso ndi Petro, Zedi uli wa awo; pakutinso uti Mgalileya.

71 Koma iye anayamba kutemberera, ndi kulumbira, Sindimdziwa munthuyu mulikunena.

72 Ndipo pomwepo tambala analira kaciwiri. Ndipo Petro anakumbukila umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ici analira misozi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16