Marko 3 BL92

Yesu aciritsa wa dzanja lopuwala

1 Ndipo analowanso m'sunagoge; ndipo munali munthu m'menemo ali ndi dzanja lace lopuwala.

2 Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamciritsa dzuwa la Sabata; kuti ammange mlandu.

3 Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati.

4 Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa dzuwa la Sabata kucita zabwino, kapena zoipa? kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala cete.

5 Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva cisoni cifukwa ca kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linacira dzanja lace.

6 Ndipo Afarisi anaturuka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye.

7 Ndipo Yesu anacokako pamodzi ndi ophunzira ace nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikuru la a ku Galileya, ndi aku Yudeya,

8 ndi a ku Yerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Y ordano, ndi a kufupi ku Turo ndi Sidoni, khamu lalikuru, pakumva zazikuruzo anazicita, linadza kwa Iye.

9 Ndipo anati kwa ophunzira ace, kuti kangalawa kamlinde Iye, cifukwa ca khamulo, kuti angamkanikize Iye,

10 pakuti adawaciritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze.

11 Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nipfuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.

12 Ndipo anailimbitsira mau kuti isamuulule Iye.

Apatula ophunzira khumi ndi awiri

13 Ndipo anakwera m'phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye.

14 Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira,

15 ndi kuti akhale nao ulamuliro wakuturutsa ziwanda.

16 Ndipo Simoni anamucha Petro;

17 ndi Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace wa Yakobo, iwo anawacha Boanerge, ndiko kuti, Ana a bingu;

18 ndi Andreya, ndi Filipo, ndi Bartolomeyo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani,

19 ndi Yudase Isikariote, ndiye amene anampereka Iye.Ndipo analowa m'nyumba.

Alembi acitira Mulungu mwano

20 Ndipo anthu ambiri anasonkhananso, kotero kuti sanathe iwo konse kudya.

21 Ndipo pamene abale ace anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaruka.

22 Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Beelzibule, ndipo, Ndi mkuru wao wa ziwanda aturutsa ziwanda.

23 Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kuturutsa Satana?

24 Ndipo ufumu ukagawanika pa uwu wokha, sukhoza kukhazikika.

25 Ndipo nyumba ikagawanika pa iyo yokha, siikhoza kukhazikika nyumbayo,

26 Ndipo Satana akadziukira mwini yekha, nagawanika, sakhoza kukhazikika, koma atsirizika.

27 Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nvumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ace, koma athange wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwace.

28 Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa macimo onse a ana a anthu, ndi zamwano ziri zonse adzacita mwano nazo;

29 koma ali yense adzacitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anaparamuladi cimo losatha;

30 pakuti adanena, Ali ndi mzimu wonyansa.

Abale ace a Yesu

31 Ndipo anadza amace ndi abale ace; naima kunja, namtumira uthenga kumuitana.

32 Ndipo anthu ambiri anakhala pansi pomzinga; nanena kwa Iye, Onani, amanu ndi abale anu ali kunja akufunani Inu.

33 Ndipo anawayankha nanena, Amai wanga ndi abale anga ndani?

34 Ndipo anawaunguza-unguza iwo akumzingawo, nanena, Taonani, amai wanga ndi abale anga.

35 Pakuti ali yense acita cifuniro ca Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16