Marko 7 BL92

Miyambo ya makolo ao

1 Ndipo anasonkhana kwa Iye Afarisi, ndi alembi ena, akucokera ku Yerusalemu,

2 ndipo anaona kuti ophunzira ace ena anadya mkate ndi m'manja mwakuda, ndiwo osasamba.

3 Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akuru;

4 ndipo pakucoka kumsika, sakudya osasamba m'thupi; ndipo ziripo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa.

5 Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akuru, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda?

6 Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa,Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao,Koma mtima wao ukhala kutari ndi ine.

7 Koma andilambira Ine kwacabe,Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.

8 Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu.

9 Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu,

10 Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo iye wakunenera zotpa atate wace kapena amai wace, afe ndithu;

11 koma inu munena, Munthu akati kwa atate wace, kapena amai wace, Karban, ndiko kuti Mtulo, cimene ukadathandizidwa naco ndi ine,

12 simulolanso kumcitira kanthu atate wace kapena amai wace;

13 muyesa acabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzicita.

14 Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani:

15 kulibe kanthu kunja kwa munthu kakulowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakuturuka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.[

16 ]

17 Ndipo m'mene Iye adalowa m'nyumba kusiyana ndi khamulo, ophunzira ace anamfunsa Iye faruzolo.

18 Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kali konse kocokera kunja kakulowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;

19 cifukwa sikalowa mumtima mwace, koma m'mimba mwace, ndipo katurukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse.

20 Ndipo anati, Coturuka mwa munthu ndico cidetsa munthu.

21 Pakuti m'kati mwace mwa mitima ya anthu, muturuka maganizo oipa, zaciwerewere,

22 zakuba, zakupha, zacigololo, masiriro, zoipa, cinyengo, cinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:

23 zoipa izi zonse zituruka m'kati, nizidetsa munthu.

Mkazi wa Suro-Fonika

24 Ndipo Iye anauka nacoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Turo ndi Sidoni, Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoza kubisika.

25 Koma pomwepo mkazi, kabuthu kace kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ace.

26 Koma mkaziyo anali Mhelene, mtundu wace MsuroFonika. Ndipo anampempha Iye kuti aturutse ciwanda m'mwana wace.

27 Ndipo ananena naye, Baleka, athange akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana ndi kuutayira tiagaru,

28 Koma iye anabvomera nanena ndi Iye, inde Ambuye; tingakhale tiagaru ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana.

29 Ndipo anati kwa iye, Cifukwa ca mau amene, muka; ciwanda caturuka m'mwana wako wamkazi.

30 Ndipo anacoka kunka kunyumba kwace, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi ciwanda citaturuka.

Yesu aciritsa munthu wogontha ndi wosalankhula

31 Ndipo anaturukanso m'maiko a ku Turo, nadzera pakati pa Sidoni, cufikira ku nyanja ya Galileya, ndi cupyola pakati pa maiko a ku Dekapolio

32 Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wacibwibwi; ndipo anampempha Iye kuti aike dzanja pa iye.

33 Ndipo anampatula pa khamu la anthu pa yekha, nalonga zala zace m'makutu mwace, nalabvula malobvu, nakhudza lilime lace:

34 nagadamira kumwamba, nausa moyo, nanena naye, Elata, ndiko, Tatseguka.

35 Ndipo makutu ace anatseguka, ndi comangira lilime lace cinamasulidwa, ndipo analankhula cilunjikire.

36 Ndipo anawalamulira kuti asauze munthu, ali yense; koma monga momwe Iye anawalamulitsa momwenso makamaka analalikira kopambana.

37 Ndipo anadabwa kwakukurukuru, nanena, Wacita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16