1 Ndipo analowanso m'sunagoge; ndipo munali munthu m'menemo ali ndi dzanja lace lopuwala.
2 Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamciritsa dzuwa la Sabata; kuti ammange mlandu.
3 Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati.
4 Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa dzuwa la Sabata kucita zabwino, kapena zoipa? kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala cete.
5 Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva cisoni cifukwa ca kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linacira dzanja lace.
6 Ndipo Afarisi anaturuka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye.
7 Ndipo Yesu anacokako pamodzi ndi ophunzira ace nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikuru la a ku Galileya, ndi aku Yudeya,