1 Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja, Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikurukuru, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m'nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m'mbali mwa nyanja.
2 Ndipo anawaphunzitsa zinthu zambiri m'mafanizo, nanena nao m'ciphunzitso cace,
3 Mverani: taonani, wofesa anaturuka kukafesa;
4 ndipo kunali, m'kufesa kwace, zina zinagwa m'mbali mwanjira, ndi mbalamezinadza ndi kuzitha kudya,