17 ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo cifukwa ca mau, pomwepo akhumudwa.
18 Ndipo ena ndiwo akufesedwa kuminga; iwo ndiwo amene adamva mau,
19 ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi cinyengo ca cuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda cipatso.
20 Ndipo iwo ofesedwa pa nthaka yabwino ndiwo oterewa akumva mau, nawalandira, nabala zipatso zakupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.
21 Ndipo ananena ndi iwo, Kodi atenga nyali kuti akaibvundikire mbiya, kapena akaiike pansi pa kama, osati kuti akaiike pa coikapo cace?
22 Pakuti kulibe kanthu kobisika, koma kuti kaonetsedwe; kapena kulibe kanthu kanakhala kam'tseri, koma kuti kakaululidwe.
23 Ngati munthu ali nao makutu akumva, amve.