28 Nthaka ibala zipatso zace yokha; uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m'ngalamo.
29 Pakucha zipatso, pamenepo atumiza zenga, pakuti nthawi yakumweta yafika.
30 Ndipo ananena, Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani?
31 Ngati mbeu yampiru, imene ikafesedwapanthaka, ingakhale icepa ndi mbeu zonse za padziko,
32 koma pamene ifesedwa, imera nikula koposa zitsamba zonse, nicita nthambi zazikuru; kotero kuti mbalame za m'mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwace.
33 Ndipo ndi mafanizo otere ambiri analankhula nao mau, 1 monga anakhoza kumva;
34 ndipo sanalankhula nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ace.