32 koma pamene ifesedwa, imera nikula koposa zitsamba zonse, nicita nthambi zazikuru; kotero kuti mbalame za m'mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwace.
33 Ndipo ndi mafanizo otere ambiri analankhula nao mau, 1 monga anakhoza kumva;
34 ndipo sanalankhula nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ace.
35 Ndipo dzuwa lomwelo, pofika madzulo, ananena kwa iwo, Tiolokere tsidya lina.
36 Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye.
37 Ndipo panauka namondwe wamkuru wa mphepo, ndi mafunde angabvira mungalawa, motero kuti ngalawa inayamba kudzala.
38 Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife?