4 ndipo kunali, m'kufesa kwace, zina zinagwa m'mbali mwanjira, ndi mbalamezinadza ndi kuzitha kudya,
5 Ndipo zina zinagwa pa nthaka yathanthwe, pamene panalibe nthaka yambiri; ndipo pomwepo zinamera, cifukwa zinalibe nthaka yakuya;
6 ndipo litakwera dzuwa zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinakhwinyata.
7 Ndipo zina zinagwa paminga, ndipominga inakula, nizitsamwitsa, ndipo sizinabala zipatso.
8 Ndipo zina zinagwa m'nthaka yabwino, ndipo zinapatsa zipatso, ndi kukula ndi kucuruka; ndipo zinabala kupindula makumi atatu, ndi makumi asanundi limodzi, ndi makumi khumi.
9 Ndipo ananena, Amene ali nao makutu akumva amve.
10 Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo.