30 Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza ziri zonse adazicita, ndi zonse adaziphunzitsa,
31 Ndipo Iye ananena nao, Idzani inu nokha padera ku malo acipululu, mupumule kamphindi, Pakuti akudza ndi akucoka anali piringu piringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.
32 Ndipo anacokera m'ngalawa kunka ku malo acipululu padera.
33 Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikila, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ocokera m'midzi monse, nawapitirira.
34 Ndipo anaturuka Iye, naona khamu lalikuru la anthu, nagwidwa cifundo ndi iwo, cifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.
35 Ndipo pamene dzuwa lidapendeka ndithu, anadza kwa Iye ophunzira ace, nanena, Malo ana nga cipululu, ndi dzuwa lapendeka ndithu;
36 muwauze kuti amuke, alowe kumiraga ndi ku midzi yozungulira, akadzigulire okha kanthu kakudya.