32 Ndipo anacokera m'ngalawa kunka ku malo acipululu padera.
33 Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikila, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ocokera m'midzi monse, nawapitirira.
34 Ndipo anaturuka Iye, naona khamu lalikuru la anthu, nagwidwa cifundo ndi iwo, cifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.
35 Ndipo pamene dzuwa lidapendeka ndithu, anadza kwa Iye ophunzira ace, nanena, Malo ana nga cipululu, ndi dzuwa lapendeka ndithu;
36 muwauze kuti amuke, alowe kumiraga ndi ku midzi yozungulira, akadzigulire okha kanthu kakudya.
37 Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya?
38 Ndipo Iye ananena nao, kuti, Muli nayo mikate ingati? pitani, mukaone. Ndipo m'mene anadziwa ananena, lsanu, ndi nsomba ziwiri.