1 Ndipo anasonkhana kwa Iye Afarisi, ndi alembi ena, akucokera ku Yerusalemu,
2 ndipo anaona kuti ophunzira ace ena anadya mkate ndi m'manja mwakuda, ndiwo osasamba.
3 Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akuru;
4 ndipo pakucoka kumsika, sakudya osasamba m'thupi; ndipo ziripo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa.
5 Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akuru, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda?