1 Masiku ajawo pakukhalanso khamu lalikuru la anthu, ndipo analibe kanthu kakudya, iye anadziitanira ophunzira ace, nanena nao,
2 Ndimva nalo cifundo khamulo, cifukwa ali ndi Ine cikhalire masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya:
3 ndipo ngati ndiwauza iwo amuke kwao osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo ena iwo acokera kutali.
4 Ndipo ophunzira ace anamyankha Iye, kuti, Munthu adzatha kutenga kuti mikate yakukhutitsa anthu awa m'cipululu muno?
5 Ndipo anawafunsa, Muli nayo mikate ingati? Ndipo anati, Isanu ndi iwiri.
6 Ndipo analamulira anthu a khamulo akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa ophunzira ace, kuti apereke kwa iwo; ndipo anapereka kwa khamulo.
7 Ndipo anali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anatidalitsa, nati atipereke itonso.