3 Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu mkazi wa Uriya Mhiti?
4 Ndipo bavide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adacoka mumsambo; ndipo anabwereranso ku nyumba yace.
5 Ndipo mkaziyo anaima, natumiza munthu nauza Davide, kuti, Ndiri ndi pakati.
6 Davide natumiza kwa Yoabu, nati, Unditumizire Uriya Mhiti. Ndipo Yoabu anatumiza Uriya kwa Davide.
7 Ndipo pakufika kwa iye Uriya uja, Davide anamfunsa kuti, Yoabu ali bwanji? ndi anthu ali bwanji? ndi nkhondo iri bwanji?
8 Ndipo Davide anauza Uriya, Utsikire ku nyumba yako, nutsuke mapazi ako, Ndipo Uriya anacoka ku nyumba ya mfumu, ndipo anamtsata munthu ndi mphatso ya mfumu.
9 Koma Uriya anagona pa khomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi anyamata onse a mbuye wace, osatsikira ku nyumba yace.