1 Ndipo kunali citapita ici, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wace wokongola, dzina lace ndiye Tamara, Amnoni mwana wa Davide anamkonda iye.
2 Ndipo Amnoni anapsinjikadi nayamba kudwala cifukwa ca mlongo wace Tamara, pakuti anali namwali, ndipo Amnoni anaciyesa capatali kumcitira kanthu.
3 Koma Amnoni anali ndi bwenzi lace, dzina lace ndiye Jonadabu, mwana wa Sineya, mbale wa Davide. Ndipo Jonadabu anali munthu wocenjera ndithu.
4 Nanena naye, Iwe mwana wa mfumu, uonderanji tsiku ndi tsiku? Sungandiuze kodi? Ndipo Amnoni anati kwa iye, Ndikonda Tamara, mlongo wa mbale wanga Abisalomu.
5 Ndipo Jonadabu ananena naye, Ugone pa kama wako ndi kudzikokomeza ulikudwala; ndipo pamene atate wako akadzakuona unene naye, Mulole mlongo wanga Tamara abwere kundipatsa kudya, nakonzere cakudyaco pamaso panga kuti ndicione ndi kucidya ca m'manja mwace.
6 Comweco Amnoni anagona, nadzikokomeza alikudwala; ndipo pamene mfumu inadza kumuona, Amnoni anati kwa mfumuyo, Mulole Tamara mlongo wanga abwere ndi kundipangira timitanda tiwiri pamaso panga, kuti ndikadye ca m'manja mwace.
7 Ndipo Davide anatumiza mau kwao kwa Tamara, kuti, Upite ku nyumba ya mlongo wako Amnoni, numkonzere cakudya,
8 Comweco Tamara anapita ku nyumba ya mlongo wace Amnoni; ndipo iye anali cigonere. Ndipo anatenga ufa naukanda naumba timitanda pamaso pace, nakazinga timitandato.
9 Ndipo anatenga ciwaya natiturutsa pamaso pace; koma anakana kudya. Ndipo Amnoni anati, Anthu onse aturuke kundisiya ine. Naturuka onse, kumsiya.
10 Ndipo Amnoni anati kwa Tamara, Bwera naco cakudya kucipinda kuti ndikadye ca m'manja mwako. Ndipo Tamara anatenga timitanda anatipangato, nabwera nato kucipinda kwa Amnoni mlongo wace.
11 Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga.
12 Koma iye anamyankha nati, lai, mlongo wanga, usandicepetsa ine, pakuti cinthu cotere siciyenera kucitika m'Israyeli, usacita kupusa kumeneku.
13 Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru m'Israyeli. Cifukwa cace tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine.
14 Koma iye sadafuna kumvera mau ace, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkangamiza, nagona naye.
15 Atatero Amnoni anadana naye ndi cidani cacikuru kopambana; pakuti cidani cimene anamuda naco, cinali cacikuru koposa cikondi adamkonda naco. Ndipo Amnoni ananena naye, Nyamuka, coka.
16 Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti coipa ici cakuti ulikundipitikitsa ncacikuru coposa cina cija unandicitira ine. Kama anakana kumvera.
17 Pomwepo anaitana mnyamata wace amene anamtumikira, nati, Turutsa mkazi uyu kwa ine, nupiringidze citseko atapita iye.
18 Ndipo iye anabvala cobvala ca mawanga mawanga, popeza ana akazi a mfumu okhala anamwali amabvala zotere. Ndipo mnyamata wace anamturutsa, napiringidza citseko atapita iye.
19 Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pace, nang'amba cobvala ca mawanga mawanga cimene analikubvala, nagwira dzanja lace pamutu pace, namuka nayenda, nalira komveka.
20 Ndipo Abisalomu mlongo wace ananena nave, Kodi mlongo wako Arononi anali ndi iwe? Koma tsopano ukhale cete, mlongo wanga, iye ali mlongo wako; usabvutika ndi cinthuci. Comweco Tamara anakhala wounguruma m'nyumba ya Abisalomu mlongo wace.
21 Koma pamene mfumu Davide anamva zonsezi, anakwiya ndithu.
22 Ndipo Abisalomu sanalankhula ndi Arononi cabwino kapena coipa, pakuti Abisalomu anamuda Amnoni, popeza adacepetsa mlongo wace Tamara.
23 Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali: nao osenga nkhosa zace ku Baalahazore pafupi pa Efraimu; ndipo Abisalomu anaitana ana amuna onse a mfumu.
24 Abisalomu nafika kwa mfumu nati, Onani, ine mnyamata, wanu ndiri nao osenga nkhosa; inu mfumu ndi anyamata anu mupite nane mnyamata wanu.
25 Ndipo mfumu inati kwa Abisalomu, lai mwana wanga, tisapite tonse, kuti tingakucurukire. Ndipo iye anaiumirira koma inakana kupita; koma inamdalitsa.
26 Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Amnoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, iye apitirenji nawe?
27 Koma Abisalomu anaiumirira iyo, nilola kuti Amnoni ndi ana amuna onse a mfumu apite naye.
28 Ndipo Abisalomu anakamulira anyamata ace, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Amnoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Amnoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, citani camuna.
29 Ndipo anyamata a Abisalomu anamcitira Amnoni monga umo Abisalomu anawalamulira. Pomwepo ana amuna onse a mfumu ananyamuka, nakwera munthu yense pa nyuru yace, nathawa.
30 Ndipo kunali akali panjira, mau anafika kwa Davide, kuti, Abisalomu anapha ana amuna onse a mfumu, osatsalapo ndi mmodzi yense.
31 Pamenepo mfumu inanyamuka ning'amba zobvala zace nigona pansi, ndipo anyamata ace onse anaimirirapo ndi zobvala zao zong'ambika.
32 Ndipo Jonadabu mwana wa Simeya mbale wa Davide anayankha nati, Mbuye wanga asaganize kuti anapha anyamata onse, ana amuna a mfumu, pakuti Amnoni yekha wafa, pakuti Ici cinatsimikizika ndi mau a Abisalomu kuyambira tsiku lija anacepetsa mlongo: wace Tamara.
33 Cifukwa cace tsono mfumu mbuye wanga asasauke mtima ndi cinthuci, ndi kuganiza kuti ana amuna onse a mfumu afa; pakuti Amnoni yekha wafa.
34 Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ace nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwace anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri.
35 Ndipo Jonadabu ananena ndi mfumu, Onani, ana amuna a mfumu afika; monga ananena mnyamata wanu, momwemo.
36 Ndipo kunali pakutsiriza iye kulankhula, onani, pomwepo ana amuna a mfumu anafika, nakweza mau ao, nalira misozi; ndi mfumu yomwe ndi anyamata ace analira ndi kulira kwakukuru ndithu.
37 Koma Abisalomu anathawa, nanka kwa Talimai mwana wa Amihuri mfumu ya ku Gesuri. Ndipo Davide analira mwana wace tsiku ndi tsiku.
38 Comweco anathawa Abisalomu, nanka ku Gesuri, nakakhala kumeneko zaka zitatu.
39 Ndipo mfumu Davide analira kunka kwa Abisalomu, cifukwa anasangalatsidwa pa imfa ya Amnoni.