2 Samueli 19 BL92

Yoabu adzudzula Davide

1 Ndipo anauza Yoabu, Onani mfumu irikulira misozi, nilira Abisalomu.

2 Ndipo cipulumutso ca tsiku lila cinasandulika maliro kwa anthu onse; pakuti anthu anamva kuti, Mfumu iri ndi cisoni cifukwa ca mwana wace.

3 Ndipo tsiku lija anthu analowa m'mudzi kacetecete, monga azemba anthu akucita manyazi pakuthawa nkhondo.

4 Ndipo mfumu inapfunda nkhope yace, nilira ndi mau okweza, Mwana wanga Abisalomu, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga,

5 Ndipo Yoabu anafika ku nyumba ya mfumu, nati, Lero mwacititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu amuna ndi akazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu ang'ono;

6 m'mene mukonda awo akudana nanu, ndi kudana nao amene akukondani. Pakuti lero mwalalikira kuti simusamalira konse akalonga ndi anyamata; pakuti lero ndizindikira kuti tikadafa ife tonse, ndipo akadakhala ndi moyo Abisalomu, pamenepo mukadakondwera ndithu.

7 Cifukwa cace tsono nyamukani, muturuke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kuturuka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo cimeneci cidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli.

8 Pamenepo mfumu inanyamuka, nikakhala pacipata, Ndipo inauza anthu kuti, Onani mfumu irikukhala pacipata; anthu onse nadza pamaso pa mfumu. Koma Aisrayeli adathawa, munthu yense ku hema wace.

9 Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israyeli analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.

10 Ndipo Abisalomu amene tinamdzoza mfumu yathu anafa kunkhondo. Cifukwa cace tsono mulekeranji kunena mau akuti abwere nayo mfumuyo?

Davide abwerera kumka ku Yerusalemu

11 Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akuru a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am'mbuyo kubwera nayo mfumu ku nyumba yace? pakuti mau a Aisrayeli onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo ku nyumba yace.

12 Inu ndinu abale anga, muli pfupa langa ndi mnofu wanga; cifukwa ninji tsono muli am'mbuyo koposa onse kubwera nayo mfumu?

13 Ndipo munene ndi Amasa, Suli pfupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala cikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yoabu.

14 Ndipo iye anakopa mitima ya anthu onse a Yuda, monga munthu mmodzi, natumiza iwo kwa mfumu, nati, Mubwere inu ndi anyamata anu onse.

15 Comweco mfumu inabwera nifika ku Yordano. Ndipo Ayuda anadza ku Giligala, kuti akakomane ndi mfumu, ndi kumuolotsa mfumu pa Yordano.

16 Ndipo Simeyi, mwana wa Gera, Mbenjammi, wa ku Bahurimu, anafulumira natsika pamodzi ndi anthu a Yuda kuti akakomane ndi mfumu Davide.

17 Ndipo anali nao anthu cikwi cimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saul; ndi ana ace amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ace makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordano pamaso pa mfumu.

18 Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kucita comkomera. Ndipo Simeyi mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordano.

19 Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukile cimene mnyamata wanu ndinacita mwamphulupulu tsiku lila mbuye wanga mfumu anaturuka ku Yerusalemu, ngakhale kucisunga mumtima mfumu.

20 Pakuti mnyamata wanu ndidziwa kuti ndinacimwa; cifukwa cace, onani, ndinadza lero, ndine woyamba wa nyumba yonse ya Yosefe kutsika kuti ndikomane ndi mbuye wanga mfumu.

21 Koma Abisai mwana wa Zeruya anayankha nati, Kodi sadzaphedwapo Simeyi cifukwa ca kutemberera wodzozedwa wa Yehova?

22 Koma Davide anati, Ndiri ndi ciani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa m'Israyeli lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israyeli lero?

23 Ndipo mfumu inanena ndi Simeyi, Sudzafa. Mfumu nimlumbirira iye.

Mefiboseti akomana ndi Davide

24 Ndipo Mefiboseti mwana wa Sauli anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasamba mapazi ace, kapena kumeta ndebvu zace, kapena kutsuka zobvalazace kuyambira tsiku lomuka mfumukufikira tsiku lobwera kwao mumtendere.

25 Ndipo kunali pakufika iye ku Yerusalemu kukakomana ndi mfumu, mfumu inanena naye, Cifukwa ninji sunapita nane Mefiboseti?

26 Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira buru kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndiri wopunduka.

27 Ndipo iye anandinamizira mnyamata wanu kwa mbuye wanga mfumu; koma mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Yehova; cifukwa cace citani cimene cikukomerani.

28 Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjeze kudandaulira kwa mfumu?

29 Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo.

30 Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere ku nyumba yace.

Barizilai akomana ndi Davide

31 Ndipo Barizilai, Mgileadi anatsika kucokera ku Rogelimu; nayambuka pa Yordano ndi mfumu, kuti akamuolotse pa Yordano.

32 Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka cakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.

33 Ndipo mfumu inanena ndi Barizilai, Tiyeni muoloke nane, ndipo ndidzakusungani pamodzi ndi ine ku Yerusalemu.

34 Koma Barizilai ananena ndi mfumu, Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kumka ku Yerusalemu?

35 Lero ndiri nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira cimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mau a amuna ndi akazi oyimba? Cifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu.

36 Mnyamata wanu angofuna kuoloka Yordano pamodzi ndi mfumu; ndipo afuniranji mfumu kundibwezerapo mphothoyotere?

37 Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mudzi wanga ku manda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Cimamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumcitire cimene cikukomerani.

38 Ndipo mfumu inayankha, Cimamu adzaoloka nane, ndipo ndidzamcitira cimene cikukomereni; ndipo ciri conse mukadzapempha kwa ine ndidzakucitirani inu.

39 Ndipo anthu onse anaoloka Yordano, ndi mfumu yomwe inaoloka; ndipo mfumuyo Inapsompsona Barizilai nimdalitsa; ndipo iye anabwerera kunka kumalo kwace.

Nsanje pakati pa Yuda ndi Israyeli

40 Comweco mfumu inaoloka nifika ku Giligala, ndi Cimamu anaoloka naye, ndipo anthu onse a Yuda adaolotsa mfumu, ndiponso gawo lina la anthu a Israyeli.

41 Ndipo onani, Aisrayeli onse anafika kwa mfumu, nanena ndi mfumu, Abale athu anthu a Yuda anakucotsani bwanji mwakuba, naolotsa mfumu ndi banja lace pa Yordano, ndi anthu onse a Davide pamodzi naye?

42 Ndipo anthu onse a Yuda anayankha anthu a Israyeli. Cifukwa mfumu iri ya cibale cathu; tsono mulikukwiyiranji pa mrandu umenewu? tinadya konse za mfumu kodi? kapena kodi anatipatsa mtulo uli wonse?

43 Ndipo anthu a Israyeli anayankha anthu a Yuda, nati, Ife tiri ndi magawo khumi mwa mfumu, ndi mwa Davide koposa inu; cifukwa ninji tsono munatipeputsa ife, osayamba kupangana nafe za kubwezanso mfumu yathu? Koma mau a anthu a Yuda anali aukali koposa mau a anthu a Israyeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24