2 Samueli 10 BL92

Davide akantha Aamoni ndi Aaramu

1 Ndipo kunali zitapita izi, mfumu ya ana a Amoni inamwalira, ndipo Hanuni mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

2 Ndipo Davide anati, Ndidzacitira Hanuni mwana wa Nahasi zokoma, monga atate wace anandicitira ine zokoma. Comweco Davide anatumiza ndi dzanja la anyamata ace kuti akamsangalatse cifukwa ca atate wace. Ndipo anyamata a Davide anafika ku dziko la ana a Amoni.

3 Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumiza anyamata ace kwa inu, kuti ayang'ane mudziwo ndi kuuzonda ndi kuupasula?

4 Comweco Hanuni anatenga anyamata a Davide nawameta ndebvu zao mbali imodzi, nadula zobvala zao pakati, kufikira m'matako ao, nawaleka amuke.

5 Pamene anaciuza Davide iye anatumiza anthu kukakomana nao; pakuti amunawo anacita manyazi akuru. Niti mfumu, Bakhalani ku Yeriko kufikira zamera ndebvuzanu; zitameramubwere.

6 Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Betirehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu cikwi cimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.

7 Ndipo pamene Davide anacimva, anatumiza Yoabu ndi khamu lonse la anthu amphamvu.

8 Ndipo ana a Amoni anaturuka, nandandalitsa nkhondo polowera kucipata. Ndipo Aaramu a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndi anthu a Tobu ndi Maaka, anali pa okha kuthengo.

9 Ndipo pamene Yoabu anaona kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, iye anasankha amuna osankhidwa onse a Israyeli, nawandandalitsa ca kwa Aramu.

10 Koma anthu otsalawo anawapereka kwa Abisai mbale wace, amene anawandandalitsa ca kwa Amoni.

11 Ndipo iye anati, Aaramu akandipambana ine, udzandithandiza ndiwe, koma ana a Amoni akapambana iwe, tsono ndidzabwera ine kukuthandiza.

12 Ulimbike mtima, ndipo ticite camuna lero cifukwa ca anthu athu ndi midzi ya Mulungu wathu; Yehova nacite comkomera.

13 Comweco Yoabu ndi anthu amene anali naye anayandikira kuponyana nkhondo ndi Aaramu. Ndipo iwowa anathawa pamaso pace.

14 Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mudzimo. Ndipo Yoabu anabwera kucokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.

15 Ndipo pamene Aaramu anaona kuti Aisrayeli anawathyola, anasonkhana pamodzi.

16 Ndipo Hadarezeri anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la cimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadarezeri anawatsogolera.

17 Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisrayeli onse, naoloka Yordano nafika ku Helemu, Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye.

18 Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israyeli; Davide naphapo Aaramu apamagareta mazana asanu ndi awiri, ndi apakavalo zikwi makumi anai, nakantha Sobaki kazembe wa khamu lao, nafa iye pomwepo.

19 Ndipo pamene mafumu onse, otumikira Hadarezeri, anaona kuti Aisrayeli anawapambana, iwo anapangana mtendere ndi Aisrayeli, nawatumikira, Comweco Aaramu anaopa kuwathandizanso ana a Amoni.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24