2 Samueli 20 BL92

Mpanduko ndi imfa ya Seba

1 Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lace ndiye Seba mwana wa Bikri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tiribe gawo mwa Davide, tiribenso colowa mwa mwana wa Jese; munthu yense apite ku mahema ace, Israyeli inu.

2 Comweco anthu onse a Israyeli analeka kutsata Davide, natsata Seba mwana wa Bikri; koma anthu a Yuda anaphatikizana ndi mfumu yao, kuyambira ku Yordano kufikira ku Yerusalemu.

3 Ndipo Davide anafika kunyumba kwace ku Yerusalemu. Mfumuyo nitenga akazi khumi ang'onowo amene adawasiya asunge nyumbayo, nawatsekera m'nyumba, nawapatsa cakudya, koma sanalowana nao. Comweco iwowa anatsekedwa kufikira tsiku la imfa yao, nakhala ngati akazi amasiye.

4 Pamenepo mfumu inati kwa Amasa, Undiitanire anthu a Yuda asonkhane asanapite masiku atatu, nukhale pano iwenso.

5 Comweco Amasa anamuka kukaitana anthu a Yuda asonkhane; koma anacedwa, napitiriza nthawi imene idamuikira.

6 Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Seba mwana wa Bikri adzaticitira coipa coposa cija ca Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze midzi ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso.

7 Ndipo anaturuka namtsata anthu a Yoabu, ndi Akereti ndi Apeleti, ndi anthu onseamphamvu; naturuka m'Yerusalemu kukalondola Seba mwana wa Bikri.

8 Pamene anafika iwo pa mwala waukuru uli ku Gibeoni, Amasa anadza kukomana nao. Ndipo Yoabu atabvala mwinjiro wace, anadzimangirira lamba lolongamo lupanga m'cimace m'cuuno mwace; ndipo m'kuyenda kwace lidasololoka.

9 Ndipo Yoabu ananena ndi Amasa, Uli bwino mbale wanga? Ndipo Yoabu anagwira ndebvu za Amasa ndi dzanja lace lamanja kuti ampsompsone.

10 Koma Amasa sanasamalira lupanga liri m'dzanja la Yoabu; comweco iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ace pansi, osamgwazanso; nafa iye, Ndipo Yoabu ndi Abisai mbale wace analondola Seba mwana wa Bikri.

11 Ndipo mnyamata wina wa Yoabu anaima pali iye, nati, Wobvomereza Yoabu, ndi iye amene ali wace wa Davide, atsate Yoabu.

12 Ndipo Amasa analikukunkhulira m'mwazi wace pakati pa mseu. Ndipo pamene munthuyo anaona kuti anthu onse anaima, iye ananyamula Amasa namcotsa pamseu kumka naye kuthengo, nampfunda ndi cobvala, pamene anaona kuti anaima munthu yense wakufika pali iye.

13 Atamcotsa iye mumseu, anthu onse anapitirira kumsata Yoabu kukalondola Seba mwana wa Bikri.

14 Ndipo anapyola mapfuko onse a Israyeli kufikira ku Abeli ndi ku Betimaaka, ndi kwa Aberi onse; iwo nasonkhana pamodzi namlondolanso.

15 Ndipo anadza nammangira misasa m'Abeli wa Betimaaka, naundira nthumbira pa mudziwo, ndipo unagunda tioga; ndipo anthu onse akukhala ndi Yoabu anakumba lingalo kuti aligwetse.

16 Pamenepo mkazi wanzeru wa m'mudzimo anapfuula, kuti, Imvani, imvani; munene kwa Yoabu, Bwerani pafupi kuno kuti ndgankhule nanu.

17 Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yoabu kodi? iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndirikumva.

18 Ndipo iye analankhula, nati, Kale adafunena kuti, Zoonadi adzapempha uphungu ku Abeli; ndipo potero mrandu udafukutha.

19 Inendine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika m'Israyeli; inu mulikufuna kuononga mudzi ndi mai wa m'Israyeli; mudzamezerang colowa ca Yehova?

20 Ndipo Yoabu anayankha nati, Iai ndi pang'ono ponse, cikhale kutali kwa ine, kuti ndingameze ndi kuononga.

21 Mranduwo soli wotere ai, koma munthu wa ku dziko lamapiri la Efraimu, dzina lace ndiye Seba mwana wa Bikri, anakweza dzanja lace pa mfumu Davide; mpereke iye yekha ndipo ndidzacoka kumudzi kuno. Ndipo mkaziyo anati kwa Yoabu, Onani tidzakuponyerani mutu wace kutumphitsa Gnga.

22 Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yace. Ndipo iwo anadula mutu wa Seba mwana wa Bikri, nauponya kunja kwa Yoabu. Ndipo analiza Gpenga, nabalalika kucoka pamudzipo, munthu yense kumka ku hema wace. Ndipo Yoabu anabwerera kumka ku Yerusalemu kwa mfumu.

23 Ndipo Yoabu anali woyang'anira khamu lonse la Israyeli; ndi Benaya, mwana wa Jehoyada, anayang'anira Akereti ndi Apeleti;

24 ndi Adoramu anayang'anira msonkho; ndi Jehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri;

25 ndi Seva anali mlembi; ndi Zadoki ndi Abyatara anali ansembe;

26 ndiponso Ira Mjairi anali nduna ya Davide.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24