1 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israyeli, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israyeli ndi Yuda.
2 Ndipo mfumu inanena ndi Yoabu kazembe wa khamu, amene anali naye, Kayendere tsopano mafuko onse a Israyeli, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, nuwerenge anthuwo, kuti ndidziwe kucuruka kwao kwa anthu.
3 Ndipo Yoabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwacurukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu acione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi cinthu ici?
4 Koma mau a mfumu anapambana Yoabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yoabu ndi atsogoleri a khamulo anaturuka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israyeli.
5 Naoloka Yordano, namanga zithando ku Aroeri ku dzanja lamanja kwa mudzi uli pakati pa cigwa ca Gadi, ndi ku Jazeri;
6 nafika ku Gileadi ndi ku dera la Tatimuhodisi; nafika ku Dani-Jaana ndi kuzungulira, kufikira ku Zidoni,
7 nafika ku linga la Turo ndi ku midzi yonse ya Ahivi ndi ya Akanani; naturukira kumwera kwa Yuda ku Beereseba.
8 Comweco pamene atayenda dziko lonse anafika ku Yerusalemu pakutha miyezi isanu ndi inai, ndi masiku makumi awiri.
9 Ndipo Yoabu anapereka kwa mfumu kucuruka kwa anthu adawawerenga; ndipo m'lsrayeli munali anthu zikwi mazana asanu ndi atatu, ngwazi zosolola lupanga; ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi mazana asanu.
10 Pamenepo mtima wa Davide unamtsutsa, atatha kuwerenga anthuwoo Davide nati kwa Yehova, Ndinacimwa kwakukuru ndi cinthu cimene ndinacita; koma tsopano Yehova mucotse mphulupulu ya mnyamata wanu, pakuti ndinacita kopusa ndithu.
11 Ndipo pouka Davide m'mawa mau a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlauli wa Davide, kuti,
12 Kalankhule ndi Davide, Atero Yehova, kuti, Ndikuikira zinthu zitatu; udzisankhire wekha cimodzi ca izo, ndikakucitire cimeneco.
13 Comweco Gadi anafika kwa Davide, namuuza, nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupitikitsani miyezi itatu? kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Cenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo.
14 Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zace nzazikuru; koma tisagwe m'dzanja la munthu.
15 Comweco Yehova anatumiza mliri pa Israyeli kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikika; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.
16 Ndipo pamene mthenga anatambasulira dzanja lace ku Yerusalemu kuuononga, coipaco cinacititsa Yehova cisoni, iye nauza mthenga wakuononga anthuwo, kuti, Kwafikira tsopano, bweza dzanja lako. Ndipo mthenga wa Yehova anali pa dwale la Arauna Mjebusi.
17 Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndacimwa ine, ndinacita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinacitanji? dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.
18 Ndipo Gadi anafika tsiku lomwelo kwa Davide nanena naye, Kwerani mukamangire Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna Mjebusi.
19 Ndipo Davide anakwerako monga mwa kunena kwa Gadi, monga adalamulira Yehova.
20 Ndipo Arauna anayang'ana naona mfumuyo ndi anyamata ace alikubwera kwa iye; naturuka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yace pansi.
21 Arauna nati, Mbuye wanga mfumu, mwadzeranji kwa mnyamata wanu? Ndipo Davide anati, Kugula dwale lako gi, kuti ndimangirepo Yehova guwa lansembe, kuti mliriwo ulekeke kwa anthu.
22 Arauna nati kwa Davide, Mbuye wanga mfumu atenge napereke nsembe comkomera; sizi ng'ombe za nsembe yopsereza, ndi zipangizo ndi zomangira ng'ombe zikhale nkhuni;
23 zonsezi, mfumu, Arauna akupatsani mfumu. Ndipo Arauna anati kwa mfumu, Yehova Mulungu wanu akulandireni.
24 Koma mfumu inati kwa Arauna, lai; koma ndidzaligula kwa iwe pa mtengo wace, pakuti sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe zopsereza zopanda mtengo wace. Momwemo Davide anagula dwalelo ndi ng'ombezo naperekapo masekeli makumi asanu a siliva.
25 Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka cifukwa ca dziko, ndi mliri wa pa Israyeli unalekeka.