1 Mafumu 1 BL92

Ukalamba wa Davide, achula Saloma wodzalowa m'malo mwace

1 NDIPO mfumu Davide anakalamba nacuruka masiku ace; ndipo iwo anampfunda ndi zopfunda, koma iye sanafundidwa.

2 Pamenepo anyamata ace ananena naye, Amfunire mbuye wanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu namsunge; nagone m'mfukato mwanu, kuti mbuye mfumu yanga afundidwe.

3 Tsono anafunafuna m'malire monse a Israyeli namwali wokongola, napeza Abisagi wa ku-Sunamu, nabwera naye kwa mfumu.

4 Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, namasunga mfumu namtumikira; koma mfumu sinamdziwa.

5 Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agareta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga.

6 Ndipo atate wace sadambvuta masiku ace onse, ndi kuti, Wlitero cifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu.

7 Ndipo anapangana ndi Yoabu mwana wa Zeruya, ndi Abyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.

8 Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wace wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simeyi, ndi Reyi, ndi anthu amphamvu aja adali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.

9 Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng'ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi citsime ca Rogeli, naitana abale ace onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anayamata a mfumu;

10 koma Natani mneneriyo, ndi Benaya, ndi anthu amphamvu aja, ndi Solomo mbale wace, sanawaitana.

11 Pamenepo Natani ananena ndi Batiseba amace wa Solomo, nati, Kodi sunamva kuti Adoniya mwana wa Hagiti walowa ufumu, ndipo Davide mbuye wathu sadziwa?

12 Ubwere tsono, ndikupangire, kuti usunge moyo wako, ndi moyo wa mwana wako Solomo.

13 Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirira mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wadfumu? ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?

14 Taona, uli cilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikiza mau ako.

15 Pamenepo Batiseba analowa kwa mfumu kucipinda; ndipo mfumuyo inali yokalamba ndithu; ndipo Abisagi wa ku Sunamu anali kutumikira mfumu.

16 Ndipo Batiseba anawerama nalambira mfumu, ndi mfumu niti, Ufunanji?

17 Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wacifumu.

18 Ndipo tsopano taonani, Adoniva walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu simudziwa.

19 Ndipo iye anapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi Abyatara wansembe, ndi Yoabu kazembe wa nkhondo; koma Solomo mnyamata wanu sanamuitana.

20 Ndipo tsopano, mbuye wanga mfumu, maso a Aisrayeli onse ali pa inu, kuti muwauze amene adzakhala pa mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye,

21 Mukapanda kutero, kudzacitika, pamene mbuye wanga mfumu atagona kwa makolo ace, ine ndi mwana wanga Solomo tidzayesedwa ocimwa.

22 Ndipo taona, iye ali cilankhulire ndi mfumu, Natani mneneriyo analowamo.

23 Ndipo anauza mfumu, kuti, Wafika Natani mneneriyo. Ndipo iye anafika pamaso pa mfumu, naweramitsa nkhope yace pansi pamaso pa mfumu.

24 Ndipo Natani anati, Mbuye wanga mfumu, kodi inu munati, Adoniya adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala ndiye pa mpando wanga wacifumu?

25 Popeza iye watsika lero, nakapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pace, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya.

26 Koma ine, inde inedi mnyamata wanu, ndi Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Solomo mnyamata wanu, sanatiitana.

27 Cinthu ici cacitika ndi mbuye wanga mfumu kodi, ndipo simunadziwitsa mnyamata wanu amene adzakhala pa mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye?

28 Tsono mfumu Davide anayankha, nati, Ndiitanireni Batiseba. Ndipo iye analowa pamaso pa mfumu, naima pamaso pa mfumu.

29 Ndipo mfumu inalumbira, niti, Pali Yehova amene anapulumutsa moyo wanga m'nsautso monse,

30 zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israyeli, ndi kuti, Zoonadi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wacifumu m'malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe.

31 Pamenepo Batiseba anaweramitsa pansi nkhope yace, nalambira mfumu, nati, Mbuye wanga mfumuakhale ndi moyo nthawi zamuyaya.

32 Ndipo mfumu Davide anati, Kandiitanireni Zadoki wansembeyo, ndi Natani mneneriyo, ndi Benaya mwana wa Yehoyada. Iwo nalowa pamaso pa mfumu.

33 Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomo mwana wanga pa nyuru yanga yanga, nimutsikire naye ku Gihoni.

34 Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israyeli; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomo akhale ndi moyo.

35 Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wacifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m'malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa lsrayeli ndi Yuda.

36 Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu.

37 Monga umo Yehova anakhalira ndi mbuye wanga mfumu, momwemo akhalenso ndi Solomo, nakuze mpando wace wacifumu upose mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu Davide.

38 Pamenepo Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja anatsika, nakweza Solomo pa nyuru ya mfumu Davide, nafika naye ku Gihoni.

39 Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali m'Cihema, namdzoza Solomo. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomo akhale ndi moyo.

40 Ndipo anthu onse anakwera namtsata, naliza zitoliro, nakondwera ndi kukondwera kwakukuru, kotero kuti pansi panang'ambikandiphokosolao.

41 Ndipo Adoniya ndi oitanidwa onse anali ndi iye analimva atatha kudya. Ndipo Yoabu, pakumva kuomba kwa lipengalo, anati, Phokosolo ndi ciani kuti m'mudzi muli cibumo?

42 iye akali cilankhulire, taona, walowa Yonatani mwana wa Abyatara wansembe, ndipo Adoniya anati, Lowa, popeza ndiwe munthu wamphamvu, nubwera nao uthenga wabwino.

43 Ndipo Yonatani anayankha, nati kwa Adoniya, Zedi Davide mbuye wathu mfumu walonga Solomo ufumu:

44 ndipo mfumu yatumanso Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja, namkweza iye pa nyuru ya mfumu.

45 Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri anamdzoza mfumu ku Gihoni, ndipo acokera kwneneko cikondwerere, ndi m'mudzimo muli phokoso. Ndilo phokoso limene mwamvali.

46 Ndiponso Solomo wakhala pa cimpando ca ufumu.

47 Ndiponso akapolo a mfumu anadzadalitsa Davide mbuye wathu mfumu, nati, Mulungu wanu aposetse dzina la Solomo lipunde dzina lanu, nakulitse mpando wace wacifumu upose mpando wanu wacifumu; ndipo mfumu anawerama pakamapo.

48 Ndiponso watero mfumu, Wolemekezeka Yehova Mulungu wa Israyeli, amene wapereka lero wina wokhala pa mpando wanga wacifumu, maso anga ali cipenyere.

49 Pamenepo oitanidwa onse a Adoniya anacita mantha, nanyamuka, napita yense njira yace.

50 Ndipo Adoniya anaopa cifukwa ca Solomo, nanyamuka, nakagwira nyanga za guwa la nsembe.

51 Ndipo anthu anakauza Solomo, kuti, Taonani, Adoniya aopa mfumu Solomo, popeza taonani, wagwira nyanga za guwa la nsembe, nati, Mfumu Solomo alumbirire ine lero kuti sadzandipha kapolo wace ndi lupanga.

52 Ndipo Solomo anati, iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lace limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye coipa, adzafadi.

53 Tsono mfumu Solomo anatuma anthu nakamtsitsa ku guwa la nsembe. Iye nadza, nagwadira mfumu Solomo; Solomo nati kwa iye, Pita kwanu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22