1 Mafumu 20 BL92

Nkhondo pakati pa Ahabu ndi Benihadadi

1 Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lace lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magareta; nakamangira Samaria misasa, naponyana nao nkhondo.

2 Natumiza mithenga lrumudzi kwa Ahabu mfumu ya Israyeli, nati kwa iye,

3 Atero Benihadadi, Siliva wako ndi golidi wako ndi wanga, akazi ako ndi ana ako omwe okometsetsawo ndi anga.

4 Ndipo mfumu ya Israyeli anayankha, nati, Monga mwanena, mbuye wanga mfumu, ndine wanu ndi zonse ndiri nazo.

5 Tsono mithenga ija inabwerera, niti, Atero Benihadadi, kuti, Ndinatumadi kwa iwe, ndi kuti, Uzindipatsa siliva wako, ndi golidi wako, ndi akazi ako, ndi ana ako;

6 koma mawa dzuwa lino ndidzatuma anyamata anga kwa iwe, nadzafunafuna m'nyumba mwako, ndi m'nyumba za anyamata ako; ndipo kudzakhala kuti cifuniro conse ca maso ako adzacigwira ndi manja ao, nadzacicotsa.

7 Pamenepo mfumu ya Israyeli anaitana akulu onse a dziko, nati, Tazindikirani inu, penyani kuti-munthu uyu akhumba coipa; popeza anatuma kwa ine kulanda akazi anga, ndi ana anga, ndi siliva, ndi golidi wanga; ndipo sindinamkaniza.

8 Ndipo akulu onse ndi anthu onse anati kwa iye, Musamvere, musabvomereze.

9 Ndipo anati kwa mithenga ya Benihadadi, Kauzeni mbuye wanga mfumu, Zonse munayamba kundituma mtumiki wanu kuzifunsa ndidzacita, koma ici sindingacicite. Nicoka mithengayo, nimbwezera mau.

10 Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati pfumbi la Samaria lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.

11 Ndipo mfumu ya Israyeli anayankha, nati, Kamuuzeni, Wakumanga zida asadzikuze ngati wakubvulayo.

12 Ndipo kunacitika, atamva Benihadadi mau awa, analikumwa nao mafumu m'misasa, ananena ndi anyamata ace, Nikani. Nandandalika pamudzipo.

13 Ndipo taonani, mneneri anadza kwa Ahabu mfumu ya Israyeli, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukuru wonse? Taonani, ndidzaupereka m'dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova.

14 Nati Ahabu, Mwa yam? Nati, Atero Yehova, Mwa anyamata a akalonga a madera. Natinso, Adzayamba kuponya nkhondo ndani? Nati, Iwe.

15 Pamenepo anawerenga anyamata a akalonga a madera, nawapeza mazana awiri mphambu makumi atatu kudza awiri. Pamenepo anawerenganso anthu onse, ndiwo ana a Israyeli onse zikwi zisanu ndi ziwiri.

16 Ndipo amenewo anaturuka usana. Koma Benihadadi analinkumwa naledzera m'misasamo, iye ndi mafumu aja makumi atatu mphambu awiri aja akumthandiza.

17 Ndipo anyamata a akalonga a madera anayamba kuturuka, koma Benihadadi anatuma anthu, iwo nambwezera mau, kuti, M'Samaria mwaturuka anthu.

18 Nati iye, Cinkana aturukira mumtendere, agwireni amoyo; cinkana aturukira m'nkhondo, agwireni amoyo.

19 Tsono anaturuka m'mudzi anyamata a akalonga a madera aja, ndi khamu la nkhondo linawatsata.

20 Ndipo ali yense anapha munthu wace; ndipo Aaramu anathawa, Aisrayeli nawapitikitsa; ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anathawira pa kavalo pamodzi ndi apakavalo.

21 Tsono mfumu ya Israyeli inaturuka, nikantha apakavalo ndi apamagareta, nawapha Aaramuwo maphedwe akuru.

22 Ndipo mneneri uja anayandikira kwa mfumu ya Israyeli, nati kwa iye, Kadzilimbitseni, mudziwe mucenjere ndi cimene mucicita; popeza caka cikudzaci mfumu ya Aramu idzabweranso kulimbana nanu.

23 Ndipo anyamata a mfumu ya Aramu anati kwa iye, Milungu yao nja kumapiri, ndimo m'mene atilakira; koma tikaponyana nao kucidikha, zedi tidzaposa mphamvu.

24 Tsono citani ici, cotsani mafumu aja yense ku malo ace, muike m'malo mwao akazembe.

25 Ndipo mudziwerengere khamu la nkhondo longa khamu lija lidaonongekalo, ndi akavalo onga akavalo aja, ndi magareta monga omwe aja; ndipo tikaponyane nao pacidikha tidzawapambana ndithu. Namvera iye mau ao, natero kumene.

26 Tsono kunacitika, pakufikanso caka Benihadadi anamemeza Aaramu nakwera ku Meld kukaponyana ndi Aisrayeli.

27 Ndipo Aisrayeli anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisrayeli anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta ana a mbuzi; koma Aaramu anadzaza dziko.

28 Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israyeli, nati, Atero: Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ici ndidzapereka unyinji uwu waukuru m'dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.

29 Ndipo awa anakhala m'misasa pandunji pa ajawo masiku asanu ndi awiri. Tsono kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri anayambana nkhondo; ndipo ana a Israyeli anaphako Aaramu tsiku limodzi anthu oyenda pansi zikwi zana limodzi.

30 Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumudzi, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mudzi, m'cipinda ca m'katimo.

31 Pamenepo anyamata ace anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israyeli ndi mafumu acifundo; tiyeni tibvale ciguduli m'cuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titurukire kwa mfumu ya Israyeli, kapena adzakusungirani moyo.

32 Motero anabvala ciguduli m'cuuno mwao, ndi zingwe pamitu pao, nafika kwa mfumu ya Israyeli, nati, Kapolo wanu Benihadadi ati, Ndiloleni ndikhale ndi moyo. Nati iye, Akali moyo kodi? Ndiye mbale wanga.

33 Tsono anthuwo anamyang'anitsa, nafulumira kugwira mauwo ngati anaterodi; nati, Mbale wanu Benihadadi ali moyo, Nati, Kamtengeni, Pamenepo Benihadadi anaturuka, nadza kwa iye, ndipo iye anamkweza m'gareta mwaceo

34 Ndipo Benihadadi anati kwa iye, Ndidzabweza midzi ija atate wanga analanda kwa atate wanu; ndipo mudzikonzere mabwalo a malonda m'Damasiko, monga umo atate wanga anadzikonzera m'Samaria. Ndi ine, ati Ahabu, ndikulola umuke ndi pangano ili. Tsono anapangana naye, namlola amuke.

35 Ndipo wina wa ana a aneneri ananena ndi mnzace mwa mau a Yehova, Undikanthe ine, Koma munthuyo anakana kumkantha.

36 Ndipo ananena naye, Popeza sunamvera mau a Yehova, taona, utalekana nane mkango udzakupha, Ndipo m'mene atalekana naye, mkango unampeza, numupha.

37 Ndipo amene uja anakomana ndi munthu wina, nati, Undikanthe. Namkantha munthuyu, namtema pomkantha.

38 Pamenepo mneneriyo anamuka, nadikira mfumu pamseu, nadzizimbaitsa ndi mpango pamaso pace.

39 Ndipo popitapa mfumu, anapfuula kwa mfumu, nati, Kapolo wanu analowa pakati pa nkhondo, ndipo taonani, munthu anapambuka nabwera ndi munthu kwa ine, nati, Tasunga munthu uyu; akasowa ndi cifukwa ciri conse moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wace, kapena udzalipa talenti la siliva.

40 Tsono pocita kapolo wanu apo ndi apo ndapeza palibe. Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa iye, Mlandu wako ukutsutsa momwemo, wadziweruza wekha.

41 Ndipo iye anafulumira kucotsa mpango kumaso kwace, ndi mfumu ya Israyeli inaona kuti anali mmodzi wa aneneri.

42 Niti kwa iye, Atero Yehova, Popeza wataya m'dzanja lako munthu uja ndinati ndimuononge konse, moyo wako udzakhala m'malo mwamoyo wace, ndi anthu ako m'malo mwa anthu ace.

43 Pamenepo mfumu ya Israyeli inamka kwao wamsunamo ndi wokwiya, nafika ku Samaria.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22