1 Mafumu 6 BL92

Za mamangidwe a Kacisi

1 Ndipo kunacitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu ataturuka ana a Israyeli m'dziko la Aigupto, caka cacinai cakukhala Solomo mfumu ya Israyeli, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi waciwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.

2 Ndipo nyumbayo mfumu Solomo anaimangira Yehova, m'litali mwace munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m'mimba mwace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mikono makumi atatu.

3 Ndipo anamanga likole pakhomo pa nyumba ya kacisiyo, m'litali mwace munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwace mwa nyumbayo, kupingasa kwace kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.

4 Ndipo m'nvumbamo anamanga mazenera a made okhazikika.

5 Ndipo anamanga zipinda zosanjikizana zogundana ndi khoma, kuzungulira makoma a nyumba ya Kacisi, ndi monenera momwemo; namanga zipinda zozinga,

6 Cipinda capansico kupingasa kwace kunali mikono isanu, capakatico kupingasa kwace mikono isanu ndi umodzi, cacitatuco kupingasa kwace mikono isanu ndi iwiri; pakuti kubwalo anacepsa khoma pozungulirapo, mitanda isalongedwe m'makoma a nyumba.

7 Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m'nyumbamo simunamveka: kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena cipangizo cacitsulo, pomangidwa iyo.

8 Khomo lolowera m'zipinda za pakati linali ku mbali ya ku dzanja lamanja ya nyumba; ndipo anthu amakwerera pa makwerero ozunguniza, kutikira ku zipinda za pakati, ndi kuturuka m'zapakatizo kulowa m'zacitatuzo,

9 Momwemo anamanga nyumbayo naitsiriza, naika mitanda, naifolera ndi matabwa amikungudza.

10 Ndipo anamanga zipindazo zogundana ndi nyumba yonseyo, cipinda ciri conse msinkhu wace mikono isanu; ndipo anazilumikizitsa kunyumba ndi mitengo yamkungudza.

11 Ndipo mau a Yehova anafika kwa Solomo, nati,

12 Kunena za nyumba yino ulikuimanga, ukamayenda iwe m'malemba anga, ndi kumacita maweruzo anga, ndi kumasunga malamulo anga onse kuyendamo, pamenepo Ine ndidzakhazikitsira iwe mau anga amene ndinauza Davide atate wako.

13 Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israyeli osawasiya anthu anga a Israyeli.

14 Tsono Solomo anamanga nyumbayo naitsiriza.

15 Ndipo anacinga makoma a nyumba m'katimo ndi matabwa amkungudza, kuyambira pansi kufikira posanja, nacinga m'katimo ndi matabwa, nayala pansi m'nyumbamo matabwa amlombwa.

16 Ndipo anadulitsa ndi matabwa amkungudza mikono makumi awiri m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwace, kuyambira pansi kulekeza kumitanda; ici anamanga m'katimo cikhale monenera, malo opatulikitsa.

17 Ndipo nyumbayo, ndiyo Kacisi wa cakuno ca monenera, inali ya mikono makumi anai.

18 Ndipo m'kati mwa nyumba munali mikungudza yosemasema, ngati zikho ndi maluwa oti gada; munali mikungudza yokha yokha simunaoneka mwala ai,

19 Ndipo anakonza monenera m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwace, kuikamo likasa la cipangano la Yehova.

20 Ndipo m'kati mwa monenera m'menemo, m'litali mwace munali mikono makumi awiri, kupingasa kwace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mikono makumi awiri; ndipo anamukuta ndi golidi woyengetsa, nakutanso guwa la nsembe ndi matabwa amkungudza,

21 Momwemo Solomo anakuta m'kati mwa nyumba ndi golidi woyengetsa, natambalika maunyolo agolidi cakuno ca monenera, namukuta ndi golidi.

22 Ndipo nyumba yonse anaikuta ndi golidi mpaka adatha nyumba yonse, ndi guwa lonse la nsembe linali cakuno ca monenera analikuta ndi golidi.

23 Ndipo m'moneneramo anasema mitengo yaazitona akerubi awiri, yense wa msinkhu wace mikono khumi.

24 Ndipo phiko limodzi la kerubi linali la mikono isanu, ndi phiko lina la kerubi linalinso la mikono isanu; kuyambira ku nsonga ya phiko limodzi kufikira ku nsonga ya phiko lina inali mikono khumi.

25 Ndi kerubi winayo msinkhu wace unali mikono khumi; akerubi onse awiri anafanana muyeso wao ndi msinkhu wao.

26 Msinkhu wa kerubi mmodzi unali mikono khumi, ndi wa kerubi wina momwemo.

27 Ndipo anaika akerubiwo m'cipinda ca m'katimo, ndi mapiko a akerubiwo anatambasuka kotero kuti phiko lace la kerubi mmodzi linajima ku khoma limodzi, ndipo phiko la kerubi wina linajima khoma lina, ndi mapiko ao anagundana pakati pa nyumba.

28 Ndipo anawakuta akerubi ndi golidi.

29 Nalemba m'makoma onse akuzinga cipinda mafano olemba ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, m'katimo ndi kumbuyo kwace.

30 Ndipo anakuta ndi golidi pansi pace pa nyumba m'katimo ndi kunja.

31 Ndipo pa khomo la monenera anapanga zitseko za mtengo waazitona, citando ca khomolo cinali limodzi la magawo asanu a khoma lace.

32 Zitseko ziwiri zomwe zinali za mtengo waazitona, anasemapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, nawakuta ndi golidi; inde anakutanso ndi golidi akerubi ndi migwalangwayo.

33 Momwemo anapanganso mphuthu zaazitona za pa khomo la Kacisi, citando cace cinali limodzi la magawo anai a khoma;

34 ndi zitseko ziwiri za mitengo yamlombwa pa khomo lina; panali citseko copatukana, ndi pa linzace panali citseko copatukana,

35 Ndipo analembapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, nakuta zolembazo ndi golidi wopsyapsyala,

36 Ndipo bwalo la m'kati analimanga mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza.

37 Maziko ace a nyumba ya Mulungu anaikidwa m'caka cacinai m'mwezi wa Zivi.

38 Ndipo m'caka cakhumi ndi cimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wacisanu ndi citatu anatsiriza nyumba konse konse monga mwa mamangidwe ace onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22