1 Mafumu 18 BL92

Eliya ndi Abaala ku Karimeli

1 Ndipo atapita masiku ambiri, mau a Yehova anafika kwa Eliya caka cacitatu, nati, Kadzionetse kwa Ahabu, ndipo ndidzatumiza mvula padziko.

2 Ndipo Eliya anamka kukadzionetsa kwa Ahabu. Ndipo njala inali yaikuru m'Samaria.

3 Ndipo Ahabu anaitana Obadiya woyang'anira nyumba yace. Koma Obadiya anaopa ndithu Yehova;

4 pakuti pamene Yezebeli anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m'phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.

5 Ndipo Ahabu anati kwa Obadiya, Kayendere dziko lonse ku zitsime zonse zamadzi, ndi ku mitsinje yonse, kapena tikapeza msipu ndi kusunga moyo wa akavalo ndi nyuru, zingafe nyama zonse.

6 Tsono iwo awiri anagawana dziko kukaliyendera; Ahabu anadzera njira yace yekha, ndi Obadiya njira yina yekha.

7 Ndipo Obadiya ali m'njira, taona, Eliya anakomana naye; iye namdziwa, namgwadira, nati, Ndinu kodi mbuye wanga Eliya?

8 Ndipo anamyankha, nati, Ndine amene; kauze mbuye wako kuti Eliya wabwera,

9 Iye nati, Ndacimwanji kuti mupereka kapolo wanu m'dzanja la Ahabu kundipha?

10 Pali Yehova Mulungu wanu, ngati kuli mtundu umodzi wa anthu, kapena ufumu, kumene mbuye wanga sanatumako kukufunani, ndipo pakunena iwo, Palibe iye, analumbiritsa ufumu umene ndi mtundu umene kuti sanakupezani.

11 Ndipo tsopano mukuti, Kauze mbuye wako kuti Eliya wabwera.

12 Ndipo kudzacitika, ine ntakusiyani, mzimu wa Yehova udzakunyamulirani kosakudziwa ine, ndipo ine ntakauza Ahabu, ndipo akalephera kukupezani, adzandipha. Koma ine kapolo wanu ndimaopa Yehova kuyambira ubwana wanga.

13 Kodi sanakuuzani mbuye wanga cimene ndidacita m'kuwapha Yezebeli aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m'phanga, ndikuwadyetsa mkate ndi madzi?

14 Ndipo tsopano inu mukuti, Kauze mbuye wako Eliya wabwera, ndipo adzandipha.

15 Koma Eliya anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndikhala pamaso pace, zedi, ndionekadi pamaso pace lero.

16 Ndipo Obadiya anauka kukomana ndi Ahabu, namuuza, ndipo Ahabu ananka kukomana ndi Eliya.

17 Ndipo kunacitika pamene Ahabu anaona Eliya, Ahabu anati kwa iye Kodi ndiwe uja umbvuta Israyeliyo?

18 Nati iye, Sindimabvuta Israyeli ine ai, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala.

19 Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisrayeli onse ku phiri la Karimeli, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a cifanizoco mazana anai, akudya pa gome la Yezebeli.

20 Pamenepo Ahabu anatumiza mau kwa ana onse a Israyeli, namemeza aneneri onse ku phiri la Karimeli.

21 Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayika-kayika kufikira liti? ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo anthu nnena kumyankha mau amodzi.

22 Ndipo Eliya ananena ndi anthuwo, Ine ndatsala ndekha mneneri wa Yehova, koma aneneri a Baala ndiwo anthu mazana anai mphambu makumi asanu.

23 Atipatse tsono ng'ombe ziwiri; ndipo adzisankhire iwo eni ng'ombe imodzi, naiduledule, naiike pankhuni osasonkhapo moto; ndipo ine ndidzakonza ng'ombe yinayo, ndi kulika pankhuni osasonkhapo moto.

24 Ndipo muitane inu dzina la mulungu wanu, ine ndidzaitana dzina la Yehova; ndipo Mulunguyo ayankhe ndi mote ndiye Mulungu. Ndipo anthu onse anabvomera, nati, Ndiwo mau abwino amene.

25 Pamenepo Eliya ananena ndi aneneri a Paala, Dzisankhireni ng'ombe imodzi yanu, muyambe kuikonza, popeza mucuruka; nimuitane dzina la mulungu wanu, koma musasonkhepo moto.

26 Ndipo iwo anatenga ng'ombe ija adawapatsa, naikonza, naitana dzina la Baala, kuyambira m'mawa kufikira pausana, nati, Baala, timvereni ife. Koma panalibe mau kapena wobvomereza. Ndipo anabvinabvina kuguwa adalimanga.

27 Ndipo pausana Eliya anawaseka, nati, Kwezani mau, popeza ndiye mulungu; kapena alikulingirira, kapena wapambuka, kapena ali paulendo, kaya agona, adzagalamuka.

28 Ndipo anakwezadi mau, nadzitema monga makhalidwe ao ndi mipeni ndi nthungo, kuti mwazi wao unali cucucu.

29 Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wobvomereza, kapena wakuwamvera.

30 Pamenepo Eliya ananena ndi anthu onse, Senderani kwa ine; ndipo onse anasendera kwa iye. Iye nakonza guwa la nsembe la Yehova lidagumukalo.

31 Ndipo Eliya anatenga miyala khumi ndi iwiri, monga mwa ciwerengo ca mafuko a ana a Yakobo, amene mau a Yehova adamfikira, kuti, Dzina lako ndi Israyeli.

32 Ndipo ndi miyalayi anamanga guwa la nsembe m'dzina la Yehova, nazunguniza guwalo ndi mcera, ukulu wace ngati kulandira miyeso iwiri ya mbeu kuzinga guwalo.

33 Ndipo anakonza nkhunizo, naduladula ng'ombe, naiika pankhuni. Nati, Dzazani madzi mbiya zinai, muwathire pa nsembe yopsereza ndi pankhuni.

34 Nati, Bwerezaninso kawiri; nabwerezanso. Nati, Bwerezani katatu; nabwereza katatu.

35 Ndipo madzi anayenda pozinga guwa la nsembe, nadzazanso meerawo ndi madzi.

36 Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isake ndi Israyeli, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israyeli, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndacita zonsezi.

37 Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti Inu mwabwezanso mitima yao.

38 Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nutentha nsembe yopsereza, ndi nkhuni, ndi miyala, ndi pfumbi, numwereretsa madzi anali mumcera.

39 Ndipo anthu onse anaona, nagwa nkhope zao pansi, nati, Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.

40 Ndipo Eliya anati kwa iwo, Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense. Nawagwira, ndipo Eliya ana pita nao ku mtsinje wa Kisoni, nawapha pamenepo.

41 Ndipo Eliya ananena ndi Ahabu, Nyamukani, idyani, imwani; popeza kumveka mkokomo: wa mvula yambiri.

42 Ndipo Ahabu anakadya, namwa; koma Eliya anakwera pamwamba pa Karimeli, nagwadira pansi, naika nkhope yace pakati pa maondo ace.

43 Ndipo anati kwa mnyamata wace, Kwera kapenyerere kunyanja. Iye nakwera, napenyetsetsa, nati, Kulibe kanthu. Nati, Bwerezanso kasanu ndi kawiri.

44 Ndipo kunali kacisanu ndi ciwiri anati, Taonani, kwaturuka kunyanja kamtambo konga dzanja la munthu. Nati iye, Kauze Ahabu, kuti, Mangani gareta, tsikani, mvula Ingakutsekerezeni.

45 Ndipo kunali, polinda kanthawi, thambo linada ndi mitambo ndi mphepo, nigwa mvula yaikuru. Ndipo Ahabu anayenda m'gareta, namuka ku Yezreeli.

46 Ndipo dzanja la Yehova tinakhala pa Eliya; namanga iye za m'cuuno mwace, nathamanga m'tsogolo mwa Ahabu ku cipata ca Yezreeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22