1 Mafumu 15 BL92

Abiya atsata zoipa za atate wace Rehabiamu

1 Ndipo caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca mfumu Yerobiamu mwana wa Nebati, Abiya analowa ufumu wa Yuda.

2 Anakhala mfumu zaka zitatu m'Yerusalemu, ndipo dzina la amace linali Maaka mwana wa Abisalomu.

3 Nayenda iye m'zoipa zonse za atate wace, zimene iye adacita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wace sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wace monga mtima wa Davide kholo lace.

4 Koma cifukwa ca Davideyo Yehova Mulungu wace anampatsa nyali m'Yerusalemu, kumuikira mwana wace pambuyo pace, ndi kukhazikitsa Yerusalemu;

5 cifukwa kuti Davide adacita colungama pamaso pa Yehova, osapambuka masiku ace onse pa zinthu zonse adamlamulira iye, koma cokhaco cija ca Uriya Mhiti.

6 Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobiamu masiku onse a moyo wace.

7 Ndipo macitidwe ace ena a Abiya, ndi zonse anazicita, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobiamu.

8 Nagona Abiya ndi makolo ace, namuika anthu m'mudzi wa Davide; Asa mwana wace nalowa ufumu m'malo mwace.

Maweruzidwe okoma a Asa

9 Ndipo caka ca makumi awiri ca Yerobiamu mfumu ya Israyeli, Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda.

10 Nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai mphambu cimodzi, ndipo dzina la amace linali Maaka mwana wa Abisalomu.

11 Ndipo Asa anacita zabwino pamaso pa Yehova monga Davide kholo lace.

12 Nacotsa m'dziko anyamata aja adama, nacotsanso mafano onse anawapanga atate ace.

13 Ndipo anamcotsera Maaka amace ulemu wa mace wa mfumu, popeza iye anapanga fano lonyansitsa likhale cifanizo; ndipo Asa analikha fano lace, nalitentha ku mtsinje wa Kidroni.

14 Koma misanje sanaicotsa, koma mtima wa Asa unali wangwiro ndi Yehova masiku ace onse.

15 Ndipo analonga m'nyumba ya Yehova zinthu zija atate wace adazipereka; napereka zinthu zina iye mwini zasiliva ndi zagolidi ndi zotengera.

Nkhondo ya pakati pa Asa ndi Basa

16 Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Basa mfumu ya Israyeli masiku ao onse.

17 Ndipo Basa mfumu ya Israyeli anakwera ndi nkhondo ku Yuda, namanga ku Rama kuwaletsa anthu asaturuke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.

18 Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golidi yense anatsala pa cuma ca nyumba ya Yehova, ndi cuma ciri m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ace; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabrimoni, mwana wa Hezroni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,

19 Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndatumiza kwa inu mphatso ya siliva ndi golidi, tiyeni lilekeke pangano liri pakati pa inu ndi Basa mfumu ya Israyeli, kuti andicokere.

20 Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa, natuma akazembe a nkhondo ace kukathira nkhondo ku midzi ya Israyeli, napasula Iyoni, ndi Dani, ndi AbeliBeti-Maaka, ndi Kineroti wonse, ndi dziko lonse la Nafitali.

21 Tsono Basa atamva izi, analeka kumanga ku Rama nakhala pa Tiriza.

22 Pamenepo mfumu Asa anamemeza Ayuda onse, osatsala ndi mmodzi yense; natuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yomwe, akamange nayo Basa; ndi mfumu Asa anamangira Geba wa ku Benjamini, ndi Mizipa.

23 Ndipo macitidwe onse ena a Asa, ndi mphamvu yace yonse, ndi zonse anazicita, ndi midzi anaimanga, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda? Koma masiku a ukalamba wace anadwala mapazi ace.

24 Nagona Asa ndi makolo ace, naikidwa kwa makolo ace m'mudzi wa Davide kholo lace; ndipo Yosafati mwana wace analowa ufumu m'malo mwace.

Basa akantha mbumba ya Yerobiamu nakhala mfumu ya Israyeli

25 Ndipo Nadabu mwana wa Yerobiamu analowa ufumu wa Israyeli caka caciwiri ca Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ya Israyeli zaka ziwiri.

26 Nacita zoipa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya atate wace, ndi m'chimo lomwelo iye akacimwitsa nalo Aisrayeli.

27 Ndipo Basa mwana wa Akiya, wa nyumba ya Isakara, anampangira ciwembu; ndipo Basa anamkanthira ku Gibetoni wa Afilisti, popeza Nadabu ndi Aisrayeli onse adamangira misasa Gibetoni.

28 Inde Basa anamupha caka cacitatu ca Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwace.

29 Tsonokunacitika, pokhalamfumu iye, anakantha nyumba yonse ya Yerobiamu, osasiyako wamoyo ndi mmodzi yense wa Yerobiamu, kufikira adamuononga monga mwa mau a Yehova, amene analankhula pa dzanja la mtumiki wace Ahiya wa ku Silo;

30 cifukwa ca macimo a Yerobiamu, amene adacimwa nao, nacimwitsa nao Aisrayeli, ndi kuutsa kwace kumene anaputa nako mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli.

31 Ndipo macitidwe ena a Nadabu, ndi zonse anazicita, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

32 Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Basa mfumu ya Israyeli masiku ao onse.

33 Tsono Basa mwana wa Ahiya analowa ufumu wa Israyeli caka cacitatu ca Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ku Tiriza zaka makomi awiri mphambu zinai.

34 Ndipo anacimwa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya Yerobiamu, ndi m'chimo lace iye anacimwitsa nalo Israyeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22