1 Mafumu 2 BL92

Davide atapangira Solomo amwalira

1 Pakuyandikira masiku ace a Davide akuti amwalire, analamulira Solomo mwana wace, nati,

2 Ndimuka ine njira ya dziko lonse: limba mtima tsono, nudzionetse umunthu;

3 nusunge cilangizo ca Yehova Mulungu wako, kuyenda m'njira zace, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wace, monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose, kuti ukacite mwa nzeru m'zonse ukacitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako;

4 kuti Yehova akakhazikitse mau ace adanenawo za ine, kuti, Ngati ana ako akasunga bwino njira zao, kuyenda moona pamaso pa Ine ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, nditi sipadzakusowa mwamuna mmodzi pa mpando wacifumu wa Israyeli.

5 Ndiponso udziwa cimene Yoabu mwana wa Zeruya anandicitira, inde cimene anawacitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israyeli, ndiwo Abineri mwana wa Neri, ndi Amasa mwana wa Yeteri, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lace la m'cuuno mwace, ndi pa nsapato za pa mapazi ace.

6 Cita mwa nzeru yako tsono, osalola mutu wace waimvi utsikire kumanda ndi mtendere.

7 Koma ucitire zokoma ana amuna aja a Barizilai wa ku Gileadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.

8 Ndipo taona uli naye Simeyi mwana wa Gera wa pfuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikuru tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordano, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga,

9 Ndipo tsono, usamuyesera iye wosacimwa, popeza ndiwe munthu wanzeru, ndipo udziwa umo uyenera kumcitira iye, nutsitsire mutu wace waimvi ndi mwazi kumanda.

10 Ndipo Davide anagona pamodzi ndi makolo ace, naikidwa m'mudzi wa Davide.

11 Ndipo masiku ace akukhala Davide mfumu ya Israyeli anali zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu ku Hebroni, ndi zaka makumi atatu mphambu citatu anakhala mfumu ku Yerusalemu.

12 Tsono Solomo anakhala pa mpando wacifumu wa Davide atate wace, ndipo ufumu wace unakhazikika kwakukuru.

Kulangidwa kwa Adoniya, Abyatara, Yoabu ndi Simeyi

13 Pomwepo Adoniya mwana wa Hagati anadza kwa Batiseba amai wace wa Solomo, ndipo mkaziyo anati, Kodi wadza ndi mtendere? Nati, Ndi mtendere umene.

14 Anatinso, Ndiri nanu mau, Nati iye, Tanena.

15 Nati iye, Mudziwa kuti ufumu unali wanga, ndi kuti Aisrayeli onse anaika maso ao pa ine, kuti ndikhale mfumu ndine; koma ufumu watembenuka nukhala wa mbale wanga, popeza iye anaulandira kwa Mulungu.

16 Ndipo tsopano, ndikupemphani pempho limodzi, musandikaniza. Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Tanena.

17 Nati iye, Mundinenere kwa mfumu Solomo, popeza sakukanizani, kuti andipatse Abisagi wa ku Sunamu akhale mkazi wanga.

18 Ndipo Batiseba anati, Cabwino, ndidzakunenera kwa mfumu.

19 Tsono Batiseba ananka kwa mfumu Solomo kukanenera Adoniya kwa iye. Ndipo mfumu inanyamuka kukomana naye, namuweramira nakhalanso pa mpando wace wacifumu, naikitsa mpando wina wa amace wa mfumu, nakhala iye ku dzanja lace lamanja.

20 Pamenepo mkaziyo anati, Ndikupemphani kapempho kamodzi, musandikaniza. Ndipo mfumu inati kwa iye, Tapemphani amai wanga, popeza sindikukanizani.

21 Ndipo iye anati, Abisagi wa ku Sunamu apatsidwe kwa Adoniya mbale wanu akhale mkazi wace.

22 Ndipo mfumu Solomo anayankha, nati kwa amai wace, Mupempheranji Abisagi wa ku Sunamu akhale wace wa Adoniya? Mumpempherenso ufumu, popeza ndiye mkuru wanga; inde ukhale wace, ndi wa Abyatara wansembeyo, ndi wa Yoabu mwana wa Zeruya.

23 Pomwepo mfumu Solomo analumbira pa Yehova, nati, Mulungu andilange naonjezepo, zedi Adoniya wadziphetsa yekha ndi mau awa.

24 Ndipo tsono, pali Yehova amene wandikhazikitsa ine, nandikhalitsa pampando wacifumu wa Davide atate wanga, nandimangira nyumba monga analonjeza, zedi Adoniya aphedwa lero lomwe.

25 Ndipo mfumu Solomo anatuma dzanja la Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo anamgwera, namwalira iye.

26 Ndipo mfumu inanena ndi Abyatara wansembeyo, Pita ku Anatoti ku minda yako; pakuti wakutidwa ndi imfa; koma sindikupha iwe lero lino, cifukwa unanyamula likasa la Ambuye Yehova pamaso pa Davide atate wanga, ndi popeza unazunzidwa monse umo atate wanga Davide anazunzidwamo.

27 Motero Solomo anacotsa Abyatara asakhalenso wansembe wa Yehova, kuti akakwaniritse mau a Yehova amene aja adalankhula ku Silo za mbumba ya Eli.

28 Ndipo mbiriyi inamfika Yoabu, pakuti Yoabu anapambukira kwa Adoniya, angakhale sanapambukira kwa Abisalomu. Ndipo Yoabu anathawira ku cihema ca Yehova, nagwira nyanga za guwa la nsembe.

29 Ndipo anamuuza mfumu Solomo, kuti, Yoabu wathawira ku cihema ca Yehova; ndipo taonani, wakhala ku guwa la nsembe. Pomwepo Solomo anatuma Benaya mwana wa Yehoyada, nati, Kamkwereo

30 Nafika Benaya ku cihema ca Yehova, nati kwa iye, Mfumu itero, Taturuka. Nati, Iai, koma ndifere pompano. Ndipo Benaya anabweza mau kwa mfumu, nati, Yoabu wanena cakuti, nandiyankha mwakuti mwakuti.

31 Ndipo mfumu inati kwa iye, Cita monga umo wanena iye, numkwere, numuike; kuti undicotsere ine ndi nyumba ya atate wanga mwazi uja Yoabu anaukhetsa wopanda cifukwa.

32 Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wace pa mutu wace wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abineri mwana wa Neri kazembe wa khamu la nkhondo la Israyeli, ndi Amasa mwana wa Yeteri kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.

33 Motero mwazi wao udzabweranso pa mutu wace wa Yoabu, ndi pa mutu wa mbumba yace, ku nthawi yamuyaya; koma Davide, ndi mbumba yace, ndi banja lace, ndi mpando wace wacifumu adzakhala ndi mtendere wa Yehova ku nthawi yamuyaya.

34 Pomwepo Benaya mwana wa Yehoyada anakwera namkantha iye, namupha; ndipo anaikidwa m'nyumba yace yace kucipululu.

35 Ndipo mfumu inaika Benaya mwana wa Yehoyada m'malo mwace kutsogolera khamu la nkhondo, ndi mfumu inaika Zadoki wansembe m'malo mwa Abyatara.

36 Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simeyi, nati kwa iye, Udzimangire nyumba m'Yerusalemu, nukhale komweko osaturukako kumka kwina konse.

37 Popeza tsiku lomwelo lakuturuka iwe ndi kuoloka mtsinje Kidroni, tadziwa ndithu kuti udzafadi, mwazi wako udzakhala pa mutu wa iwe wekha.

38 Ndipo Simeyi ananena ndi mfumu, Mau awa ndi abwino; monga momwe mwanena mbuye wanga mfumu momwemo ndidzacita kapolo wanu. Ndipo Simeyi anakhala m'Yerusalemu masiku ambiri.

39 Ndipo kunacitika, zitapita zaka zitatu, kuti akapolo awiri a Simeyi anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka mfumu ya Gati. Ndipo anamuuza Simeyi, nati, Taonani, akapolo anu akhala ku Gati.

40 Ndipo Simeyi ananyamuka, namangirira mbereko pa buru wace, namka ku Gati kwa Akisi kukafuna aka polo ace; namuka Simeyi, nabwera nao akapolo ace kucokera ku Gati.

41 Ndipo anamuuza Solomo, kuti, Simeyi wacoka ku Yerusalemu kumka ku Gati, nabweranso.

42 Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simeyi, niti kwa iye, Kodi sindinakulumbiritsa pa Yehova ndi kukucenjeza, kuti, Tadziwa ndithu, kuti tsiku lakuturuka iwe ndi kukayenda kwina konse udzafa ndithu? Ndipo iwe unati kwa ine, Mau amene ndawamva ndi abwino.

43 Sunasunga cifukwa ninji lumbiro la pa Yehova, ndi lamulo lija ndinakulamulira iwe?

44 Tsono mfumu inanenanso ndi Simeyi, Udziwa iwe coipa conse mtima wako umadziwaco, cimene udacitira Davide atate wanga; cifukwa cace Yehova adzakubwezera coipa cako pamutu pako mwini.

45 Koma mfumu Solomo adzadalitsika, ndi mpando wacifumu wa Davide udzakhazikika pamaso pa Yehova ku nthawi yamuyaya.

46 Pamenepo mfumu inalamulira Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye anaturuka namkwera, namwalira iye. Ndipo ufumu unakhazikika m'dzanja la Solomo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22