1 Mafumu 21 BL92

Yezebeli aphetsa Naboti

1 Ndipo zitatha izi, kunaoneka zotere: Naboti wa ku Yezreeli anali ndi munda wamphesa, unali m'Yezreelimo, m'mbali mwa nyumba ya Ahabu mfumu ya ku Samaria.

2 Ndipo Ahabu analankhula ndi Naboti, nati, diloleni Ndipatse munda wako wamphesa ukhale munda wanga wa ndiwo, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga; ndipo m'malo mwace ndidzakupatsa munda wamphesa wokoma woposa uwu; kapena kukakukomera ndidzakupatsa ndalama za pa mtengo wace,

3 Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang'ono ponse ai, kuti ndikupatseni colowa ca makolo anga,

4 Ndipo Ahabu analowa m'nyumba mwace wamsunamo ndi wokwiya, cifukwa ca mau amene Naboti wa ku Yezreeli adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani colowa ca makolo anga. M'mwemo anagona pa kama wace, nayang'ana kumbali, nakana kudya mkate.

5 Koma Yezebeli mkazi wace anadza kwa iye, nati kwa iye, Mucitiranji msunamo, kuti mukana kudya mkate?

6 Nati kwa iye, Popeza ndinalankhula kwa Naboti wa ku Yezreeli, ndinati kwa iye, Undigulitse munda wako ndi ndalama; kapena ukafuna, ndikupatsa munda wina m'malo mwace; kama anandiyankha, Sindikupatsani munda wanga wamphesa.

7 Ndipo Yezebeli mkazi wace anati kwa iye, Kodi mulamulira Aisrayeli tsopano ndinu? Taukani, idyani mkate, ukondwere mtima wanu; munda wa Naboti wa ku Yezreeli ndidzakupatsani ndine.

8 M'mwemo analemba akalata m'dzina la Ahabu nakhomerapo cizindikilo cace, natumiza akalatawo kwa akulu ndi omveka anali m'mudzi mwace, nakhala naye Naboti.

9 Ndipo analemba m'akalata, nati, Lalikirani kuti asale kudya, muike Naboti pooneka ndi anthu;

10 ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pace, kuti amcitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumturutse ndi kumponya miyala kumupha.

11 Ndipo anthu aja a mudzi wace, ndiwo akulu ndi omveka adakhala m'mudzi mwace, anacita monga Yezebeli anawatumizira, monga munalembedwa m'akalata amene iye anawatumizira.

12 Analalikira kuti asale kudya, naike Naboti pooneka ndi anthu.

13 Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pace, ndipo anthu oipawo anamcitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamturutsa m'mudzi, namponya miyala, namupha.

14 Pomwepo anatuma mau kwa Yezebeli, nati, Naboti waponyedwa miyala, nafa.

15 Ndipo kunali, atamva Yezebeli kuti anamponya Naboti miyala nafa, Yezebeli anati kwa Ahabu, Taukani, landirani munda wamphesa wa Naboti Myezreeli uja anakana kukugulitsani ndi ndarama, popeza, Naboti sali ndi moyo, koma wafa.

16 Ndipo kunali, atamva Ahabu kuti Naboti wafa, Ahabu anauka kukatsikira ku munda wamphesa wa Naboti, kuulandira.

Eliya auza Ahabu za kuonongeka kwa mbumba yace

17 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Eliya waku Tisibe, nati,

18 Nyamuka, tsikira kukakomana ndi Ahabu mfumu ya Israyeli, akhala m'Samariya; taona, ali ku munda wamphesa wa Naboti kumene anatsikira kukaulandira.

19 Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, mulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agaru ananyambita mwazi wa Naboti, pompaja agaru adzanyambita mwazi wako, inde wako.

20 Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kucita coipaco pamaso pa Yehova.

21 Taona, ndidzakufikitsira coipa, ndi kucotsa mbumba yako psiti; ndipo ndidzalikhira Ahabu mwana wamwamuna yense, ndi yense womangika ndi womasuka m'lsrayeli;

22 ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobiamu mwana wa Nebati, ndi ya Basa mwana wa Ahiya; cifukwa ca kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kucimwitsa Israyeli.

23 Ndipo za Yezebeli yemwe Yehova ananena, nati, Agaru adzadya Yezebeli ku linga la Yezreeli.

24 Mwana ali yense wa Ahabu amene adzafera m'mudzi, agaru adzamudya; ndipo iye amene adzafera kuthengo, mbalame za m'mlengalenga zidzamudya,

25 Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kucita coipa pamaso pa Yehova, amene Yezebeli mkazi wace anamfulumiza.

26 Ndipo anacita moipitsitsa kutsata mafano, monga mwa zonse amazicita Aamori, amene Yehova adawapitikitsa pamaso pa ana a Israyeli.

27 Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang'amba zobvala zace, nabvala ciguduli pathupi pace, nasala kudya, nagona paciguduli, nayenda nyang'anyang'a.

28 Pamenepo mau a Yehova anadza kwa Eliya wa ku Tisibe, nati,

29 Waona umo wadzicepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzicepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa coipa cimeneci akali moyo iye; koma m'masiku a mwana wace ndidzacifikitsa pa nyumba yace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22