1 Ndipo mfumu Solomo anali mfumu ya Israyeli yense.
2 Ndipo akuru a mfumu ndi awa: Azariya mwana wa Zadoki anali nduna,
3 Elihorepa ndi Ahiya ana a Sisa alembi, Yehosafati mwana wa Ahiludi wolembera mbiri,
4 ndi Benaya mwana wa Yehoyada anali kazembe wa nkhondo, ndi Zadoki ndi Abyatara anali ansembe,
5 ndi Azariya mwana wa Natani anayang'anira akapitao, ndi Zabudi mwana wa Natani anali nduna yopangira mfumu,
6 ndi Ahisara anayang'anira banja la mfumu, ndi Adoniramu mwana wa Abida anali wamsonkho.
7 Ndipo Solomo anali nao akapitao khumi ndi awiri akuyang'anira Aisrayeli onse, akufikitsira mfumu ndi banja lace zakudya; ali yense anafikitsa zakudya zofikira mwezi umodzi wa caka.
8 Ndipo maina ao ndiwo: Benhuri anatengetsa ku mapiri a Efraimu;
9 Bendekeri ku Makazi ndi Saalibimu ndi Betsemesi ndi Elonibetanani;
10 Benhesedi ku Aruboti ndi Soko ndi dziko lonse la Heferi;
11 Benabinadabu ku mtunda wa Dori, mkazi wace ndiye Tafati mwana wa Solomo;
12 Baana mwana wa Ahiludi ku Tanaki ndi Megido ndi Betseani konse, ali pafupi ndi Zaratana kunsi kwa Yezreeli, kuyambira ku Betseani kufikira ku Abelimehola, kufikiranso kundunji ku Yokineamu;
13 Benigeheri ku Ramoti Gileadi, iyeyo anali nayo midzi ya Yairo mwana wa Manase iri m'Gileadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobi liri m'Basani, midzi yaikuru makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;
14 Abinadabu mwana wa Ido ku Nahanaimu;
15 Ahimazi ku Nafitali, iyeyu adakwatira Basemati mwana wa Solomo;
16 Baana mwana wa Husayi ku Aseri ndi ku Aloti;
17 Yehosafati mwana wa Paruwa ku Isakara;
18 Simeyi mwana wa Ela ku Benjamini;
19 Geberi mwana wa Uri ku dziko la Gileadi, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi la Ogi mfumu ya Basani; munalibe kapitao wina m'deramo.
20 Ayuda ndi Aisrayeli anacuruka ngati mcenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.
21 Ndipo Solomo analamulira maiko onse, kuyambira ku Firate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Aigupto; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomo masiku onse a moyo wace.
22 Ndipo zakudya za Solomo zofikira tsiku limodzi zinalr miyeso makumi atatu ya ufa wosalala, ndi miyeso makumi asanu ndi limodzi ya ufa wamankhupete,
23 ng'ombe zonenepa khumi, ndi ng'ombe za kubusa makumi awiri, ndi nkhosa zana limodzi, osawerenganso ngondo ndi nswala ndi mphoyo ndi mbalame zoweta.
24 Pakuti analamulira dziko lonse liri tsidya lino la Firate, kuyambira ku Tipsa kufikira ku Gaza, inde mafumu onse a ku tsidya tino la Firate; nakhala ndi mtendere kozungulira konseko,
25 Ndipo Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wace ndi mkuyu wace, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.
26 Ndipo Solomo anali nazo zipinda za akavalo a magareta ace zikwi makumi anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri.
27 Ndipo akapitao aja anatengetsera cakudya Solomo ndi anthu onse akudya ku gome la mfumu Solomo, munthu yense m'mwezi mwace, sanalola kanthu kasoweke.
28 Barelenso ndi udzu wa akavalo ndi ngamila anabwera nazo kumalo kwao, munthu yense monga momwe anamuuzira.
29 Ndipo Mulungu anampatsa Solomo nzeru ndi luntha lambiri, ndi mtima wodziwa za mitundu mitundu, zonga mcenga uli m'mbali mwa nyanja.
30 Ndipo nzeru ya Solomo inaposa nzeru za anthu onse a kum'mawa, ndi nzeru zonse za ku Aigupto.
31 Pakuti anali wanzeru woposa anthu onse, woposa Etani wa ku Ezra, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Darida ana a Maholi; ndipo mbiri yace inafikira amitundu onse ozungulira.
32 Ndipo ananena miyambo zikwi zitatu, ndipo nyimbo zace zinali cikwi cimodzi mphambu zisanu.
33 Nakamba za mitengo, kuyambira mkungudza uli ku Lebano kufikira hisopi wophuka pakhoma; anakambanso za nyama ndi mbalame ndi zinthu zokwawa pansi ndi za nsomba.
34 Ndipo anafikako anthu a mitundu yonse kudzamva nzeru ya Solomo, ocokera kwa mafumu onse a dziko lonse lapansi, amene adamva mbiri ya nzeru yace.