1 Mafumu 14 BL92

Ahiya aneneratu kugwa kwa Yerobiamu

1 Nthawi yomweyo Abiya mwana wa Yerobiamu anadwala.

2 Ndipo Yerobiamu ananena ndi mkazi wace, Unyamuke, nudzizimbaitse, ungadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yerobiamu, nupite ku Silo; taona, kumeneko kuli Ahiya mneneri uja anandiuza ine ndidzakhala mfumu ya anthu awa.

3 Nupite nayo mikate khumi, ndi timitanda, ndi cigulu ca uci, numuke kwa iye; adzakuuza m'mene umo akhalire mwanayo.

4 Natero mkazi wa Yerobiamu, nanyamuka namka ku Silo, nalowa m'nyumba ya Ahiya. Koma Ahiya sanatha kupenya, popeza maso ace anali tong'o, cifukwa ca ukalamba wace.

5 Ndipo Yehova ananena ndi Ahiya, Taona, mkazi wa Yerobiamu akudza kukufunsa za mwana wace, popeza adwala; udzanena naye mwakuti mwakuti; popeza kudzakhala pakulowa iye adzadzizimbaitsa.

6 Ndipo kunacitika, pamene Ahiya anamva mgugu wa mapazi ace alinkulowa pakhomo, anati, Lowa mkazi iwe wa Yerobiamu, wadzizimbaitsiranji? pakuti ine ndatumidwa kwa iwe ndi mau olasa.

7 Kauze Yerobiamu, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ndingakhale ndinakukulitsa pakati pa anthu, ndi kukukhalitsa mfumu ya anthu anga Aisrayeli,

8 ndipo ndinalanda nyumba ya Davide ufumu, ndi kuupereka kwa iwe, koma sunafanana ndi Davide mtumiki wanga uja, amene anasunga malamulo anga, nanditsata ndi mtima wace wonse kucita zolunjika zokha zokha pamaso panga;

9 koma wacimwa koposa onse akale, nukadzipangira milungu yina ndi mafano yoyenga kundikwiyitsa, nunditaya Ine kumbuyo kwako;

10 cifukwa cace, taona, ndidzafikitsa coipa pa nyumba ya Yerobiamu, ndi kugurula mwana wamwamuna yense wa Yerobiamu womangika ndi womasuka m'Israyeli, ndipo ndidzacotsa psiti nyumba yonse ya Yerobiamu, monga munthu acotsa ndowe kufikira idatha yonse.

11 Agaru adzadya ali yense wa Yerobiamu wakufa m'mudzi; ndi mbalame za m'mlengalenga zidzadya yense wakufera kuthengo; popeza wanena ndi Yehova.

12 Tanyamuka tsono, numuke kwanu; pakulowa mapazi ako m'mudzi mwanayo adzatsirizika.

13 Ndipo Aisrayeli onse adzamlira, nadzamuika, popeza iye yekha wa ana a Yerobiamu adzalowa m'manda; pakuti mwa iye mwapezedwa cokoma ca kwa Yehova Mulungu wa Israyeli m'nyumba ya Yerobiamu.

14 Ndiponso Yehova adzadziukitsira mfumu ya Israyeli, idzaononga nyumba ya Yerobiamu tsiku lomwelo; nciani ngakhale tsopano apa?

15 Popeza Yehova adzawakantha Aisrayeli monga bango ligwedezeka ndi madzi, nadzazula Aisrayeli m'dziko lino labwino analipatsa makolo ao, nadzawamwazira ku tsidya lija la Firate, popeza iwo anapanga zifanizo zao zokwiyitsa Yehova.

16 Ndipo adzai pereka Aisrayeli cifukwa ca macimo a Yerobiamu anacimwawo, nacimwitsa nao Aisrayeli.

17 Ndipo mkazi wa Yerobiamu ananyamuka nacoka, nafika ku Tiriza; ndipo polowa iye pa khomo la nyumba yace anatsirizika mwanayo.

18 Ndipo anamuika, namlira Aisrayeli, monga mwa mau a Yehova anawalankhula pa dzanja la mtumiki wace Ahiya mneneri.

19 Ndipo macitidwe ena a Yerobiamu m'mene umo anacitira nkhondo, ndi m'mene umo anacitira ufumu, taona, analembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.

20 Ndipo masiku akukhala Yerobiamu mfumu anali zaka makumi awiri mphambu ziwiri, nagona iye kwa makolo ace, nalowa ufumu m'malo mwace Nadabu mwana wace.

Yuda aipsidwa mwa Rehabiamu

21 Ndipo Rehabiamu mwana wa Solomo anali mfumu ya dziko la Yuda. Rehabiamu anali wa zaka makumi anai mphambu cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, m'mudzi m'mene Yehova adausankha m'mafuko onse a Israyeli kukhazikamo dzina lace. Ndipo dzina la amace linali Naama M-amoni.

22 Ndipo Ayuda anacita zoipa pamaso pa Yehova, namcititsa nsanje ndi zoipa zao anazicitazo, zakuposa zija adazicita makolo ao,

23 Pakuti anadzimangiranso misanje, ndi zoimiritsa, ndi zifanizo, pa citunda conse cacitali, ndi patsinde pa mtengo wogudira uli wonse;

24 panalinso anyamata ocitirana dama m'dzikomo; iwo amacita monga mwa zonyansitsa za amitundu, amene Yehova anapitikitsa pamaso pa ana a Israyeli.

25 Ndipo kunacitika, Rebabiamu atakhala mfumu zaka zisanu, Sisaki mfumu ya Aigupto anakwera ndi nkhondo ku Yerusalemu,

26 nacotsa cuma ca m'nyumba ya Yehova, ndi cuma ca m'nyumba ya mfumu; inde anacotsa conseco, nacotsanso zikopa zagolidi zonse adazipanga Solomo.

27 Ndipo mfumu Rehabiamu anapanga m'malo mwa izo zikopa zina zamkuwa, nazipereka m'manja a akapitao a olindirira, akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.

28 Ndipo kunacitika, pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, olindirira aja anazinyamula, nabweranso nazo ku cipinda ca olindirirawo.

29 Tsono, macitidwe ace ena a Rehabiamu, ndi zonse anazicita, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

30 Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehabiamu ndi Yerobiamu masiku ao onse.

31 Nagona Rehabiamu ndi makolo ace, naikidwa kwa makolo ace m'mudzi wa Davide. Ndipo dzina la amace linali Naama M-amoni, nalowa ufumu m'malo mwace Abiya mwana wace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22