1 Ndipo Solomo anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aigupto, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye ku mudzi wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu.
2 Koma anthu anaphera nsembe pamisanje, popeza panalibe nyumba yomangira dzina la Yehova kufikira masiku omwewo.
3 Ndipo Solomo anakondana ndi Yehova, nayenda m'malemba a Davide atate wace; koma anaphera nsembe nafukiza zonunkhira pamisanje.
4 Ndipo mfumu inapita ku Gibeoni kukaphera nsembe kumeneko; popeza msanje waukuru unali kumeneko, Solomo anapereka nsembe zopsereza cikwi cimodzi pa guwalo la nsembe.
5 Ku Gibeoni Yehova anaonekera Solomo m'kulota usiku, nati Mulungu, Tapempha cimene ndikupatse.
6 Ndipo Solomo anati, Munamcitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi coonadi ndi cilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira cokoma ici cacikuru kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wace wacifumu monga lero lino.
7 Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m'malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kuturuka kapena kulowa.
8 Ndipo kapolo wanu ndiri pakati pa anthu anu amene Inu munawasankha, anthu ambirimbiri osawerengeka, kapena kulembeka m'unyinji wao.
9 Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?
10 Ndipo mau amenewa anakondweretsa Yehova kuti Solomo anapempha cimeneci.
11 Ndipo Mulungu anati kwa iye, Popeza wapempha cimeneci, osadzipemphera masiku ambiri, osadzipempheranso cuma, osadzipempheranso moyo wa adani ako, koma wadzipemphera nzeru zakumvera mirandu;
12 taona, ndacita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka.
13 Ndiponso zimene sunazipempha adakupatsa, ndipo cuma ndi ulemu, kuti pakati pa mafumu sipadzakhala yina yolingana ndi iwe masiku ako onse.
14 Ndipo ukadzayenda m'njira zanga kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga atate wako Davide anayendamo, Ine ndidzacurukitsa masiku ako.
15 Ndipo Solomo anauka, ndipo taona, ndilo loto; nabwera ku Yerusalemu, naima ku likasa la cipangano ca Yehova, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere, nakonzera anyamata ace onse madyerero.
16 Pamenepo analowa kwa mfumu akazi awiri, ndiwo adama, naima pamaso pace.
17 Ndipo mkazi mmodzi anati, Mbuye wanga, ine ndi mkazi uyu tikhala awiri m'nyumba imodzi; ndipo ine ndinaona mwana, iye ali m'nyumbamo.
18 Ndipo kunacitika kuti tsiku lacitatu nditaona ine mwana, mnzangayu anaonanso mwana; ndipo ife tinali pamodzi, munalibe mlendo ndi ife m'nyumbamo, koma ife awiri m'nyumbamo.
19 Ndipo mwana wa mnzangayu anamwalira usiku, pokhala iyeyu anamgonera.
20 Ndipo iye anauka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga, mdzakazi wanu ndiri m'tulo, namuika m'mfukato mwace, naika mwana wace wakufa m'mfukato mwanga.
21 Ndipo pouka ine m'mawa kuyamwitsa mwana wanga ndaona ngwakufa, koma nditamzindikira m'mawa ndaona si mwana wanga wobala ine ai.
22 Ndipo mkazi winayo anati, lai, koma wamoyoyu ndi mwana wanga, ndi wakufayu ndi mwana wako. Ndipo uja anati, lai, koma wakufayu ndi mwana wako, ndi wamoyoyu ndi mwana wanga. Motero iwo analankhula pamaso pa mfumu.
23 Tsono mfumu inati, Uyu akuti, Wamoyoyu ndiye mwana wanga ndi wakufayu ndiye mwana wako; ndipo winayo akuti, lai, koma mwana wako ndiye wakufayu, ndi mwana wanga ndiye wamoyoyu.
24 Niti mfumu, Kanaitengereni cimpeni. Ndipo iwo anabwera ndi cimpeni kwa mfumu.
25 Mfumu niti, Dula pakati mwana wamoyoyu, nupatse mmodzi cipinjiri, ndi wina cipinjiri cace.
26 Koma mkazi amene mwana wamoyo anali wace analankhula ndi mfumu, popeza mtima wace unalira mwana wace, nati, Ha! mbuye wanga, mumpatse uyo mwana wamoyo osamupha konse. Koma winayo anati, Asakhale wanga kapena wako, dulani.
27 Pamenepo mfumu inayankha, niti, Mumpatse wacifundoyo mwana wamoyo, osamupha konse, uyo ndiye amace.
28 Ndipo Aisrayeli onse anamva maweruzidwe ace idaweruza mfumu, naopa mfumu; pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye yakuweruza.