1 Mafumu 9 BL92

Mulungu aonekanso kwa Solomo

1 Ndipo kunali, atatsiriza Solomo kumanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi cifuniro conse ca Solomo anacikhumbaco,

2 Yehova anaonekera kwa Solomo nthawi yaciwiri, monga momwe adamuonekera ku Gibeoni.

3 Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.

4 Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga, monga momwe Davide atate wako anayendera ndi mtima woona ndi wolungama, kuzicita zonse ndakulamulirazo, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga,

5 pamenepo Ine ndidzakhazikitsa cimpando ca ufumu wako pa Israyeli nthawi yosatha, monga ndinalonjezana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wamwamuna pa mpando wacifumu wa Israyeli.

6 Koma mukadzabwerera pang'ono pokha osanditsata, kapena inu, kapena ana anu, osasunga malamulo anga ndi malemba anga amene ndawaika pamaso panu; mukadzatumikira milungu yina ndi kuilambira;

7 pamenepo Ine ndidzalikha Aisrayeli kuwacotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba yino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israyeli adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.

8 Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali yino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero cifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba yino?

9 Ndipo anthu adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wao amene adaturutsa makolo ao m'dziko la Aigupto, natsata milungu yina, nailambira, naitumikira; cifukwa cace Yehova anawagwetsera coipa conseci.

Za midzi adaimanga Saloma, ndi zomba zace

10 Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomo adatsiriza nyumba ziwirizo, ndizo nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu;

11 popeza Hiramu mfumu ya Turo adamthandiza Solomo ndi mitengo yamkungudza ndi yamlombwa ndi golidi yemwe, monga momwe iye anafuniramo, cifukwa cace mfumu Solomo anampatsa Hiramu midzi makumi awiri m'dziko la Galileya.

12 Ndipo Hiramu anaturuka ku Turo kukaona midzi adampatsa Solomoyo, koma siinamkomera.

13 Nati, Midzi yino mwandipatsayi njotani, mbale wanga? Naicha dzina lao, Dziko lacikole, kufikira lero lino.

14 Ndipo Hiramu adatumiza kwa mfumu matalenti a golidi zana limodzi mphambu makumi awiri.

15 Ndipo cifukwa cace ca msonkho uja anausonkhetsa mfumu Solomo ndi cimeneci; kuti amange nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya iye yekha, ndi Milo, ndi linga la Yerusalemu, ndi Hazori, ndi Megido; ndi Gezeri.

16 Pakuti Farao mfumu ya Aigupto adakwera nalanda Gezeri, nautentha ndi moto, nawapha Akanani akukhala m'mudzimo, naupereka kwaulere kwa mwana wace mkazi wa Solomo.

17 Ndipo Solomo anamanganso Gezeri, ndi Betihoroni wakunsi,

18 ndi Balati, ndi Tadimori wa m'cipululu m'dziko muja,

19 ndi midzi yonse yosungamo zinthu zace za Solomo, ndi midzi yosungamo magareta ace, ndi midzi yokhalamo apakavalo ace, ndi zina ziti zonse zidakomera Solomo kuzimanga m'Yerusalemu, ndi ku Lebano, ndi m'dziko lonse la ufumu wace.

20 Ndipo Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi otsala, amene sanali a ana a Israyeli,

21 ana ao amene adatsala m'dziko, amene ana a lsrayeli sanakhoza kuononga konse, Solomo anawasenzetsa msonkho wa nchito kufikira lero.

22 Koma Solomo sanawayesa ana a Israyeli akapolo, koma iwowo anali anthu a nkhondo, ndi anyamata ace, ndi akalonga ace, ndi akazembe ace, ndi oyang'anira magareta ace ndi apakavalo ace.

23 Ameneyo anali akulu a akapitao oyang'anira nchito ya Solomo, mazana asanu mphambu makumi asanu akulamulira anthu ogwira nchito aja.

24 Koma mwana wamkazi wa Farao anaturuka m'mudzi wa Davide kukwera ku nyumba yace adammangira Solomo, pamenepo iye anamanganso Milo.

25 Ndipo caka cimodzi Solomo anapereka katatu nsembe zopsereza ndi zamtendere, pa guwa la nsembe limene anammangira Yehova, nafukiza zonunkhira pa guwa la nsembe pamaso pa Yehova, atatsiriza nyumbayo.

26 Ndipo mfumu Solomo anamanga zombo zambiri ku Ezioni Geberi uli pafupi ndi Eloti, pambali pa Nyanja Yofiira, ku dziko la Edomu.

27 Ndipo, Hiramu anatuma anyamata ace m'zombozo amarinyero ozerewera m'nyanja, pamodzi ndi anyamata a Solomo.

28 Ndipo iwo anafika ku Ofiri, natengako golidi matalenti mazana anai mphambu makumi awiri, nafika naye kwa mfumu Solomo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22